< Masalimo 58 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama? Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu? 2 Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama, ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi. 3 Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera; kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza. 4 Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka, ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake. 5 Imene simva liwu la munthu wamatsenga, ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo. 6 Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu, Yehova khadzulani mano a mikango! 7 Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa. 8 Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda; ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa. 9 Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku, kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa. 10 Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango, pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa. 11 Ndipo anthu adzanena kuti, “Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho; zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”

< Masalimo 58 >