< Masalimo 50 >

1 Salimo la Asafu. Wamphamvuyo, Yehova Mulungu, akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
מזמור לאסף אל אלהים יהוה-- דבר ויקרא-ארץ ממזרח-שמש עד-מבאו
2 Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri Mulungu akuwala.
מציון מכלל-יפי-- אלהים הופיע
3 Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete; moto ukunyeketsa patsogolo pake, ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
יבא אלהינו ואל-יחרש אש-לפניו תאכל וסביביו נשערה מאד
4 Iye akuyitanitsa zamumlengalenga ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
יקרא אל-השמים מעל ואל-הארץ לדין עמו
5 Mundisonkhanitsire okhulupirika anga, amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
אספו-לי חסידי-- כרתי בריתי עלי-זבח
6 Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake, pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.
ויגידו שמים צדקו כי-אלהים שפט הוא סלה
7 Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula, iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa; ndine Mulungu, Mulungu wako.
שמעה עמי ואדברה-- ישראל ואעידה בך אלהים אלהיך אנכי
8 Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako, kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
לא על-זבחיך אוכיחך ועולתיך לנגדי תמיד
9 Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako kapena mbuzi za mʼkhola lako,
לא-אקח מביתך פר ממכלאתיך עתודים
10 pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
כי-לי כל-חיתו-יער בהמות בהררי-אלף
11 Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
ידעתי כל-עוף הרים וזיז שדי עמדי
12 Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
אם-ארעב לא-אמר לך כי-לי תבל ומלאה
13 Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna kapena kumwa magazi a mbuzi?
האוכל בשר אבירים ודם עתודים אשתה
14 “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu, kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
זבח לאלהים תודה ושלם לעליון נדריך
15 Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso; Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”
וקראני ביום צרה אחלצך ותכבדני
16 Koma kwa woyipa, Mulungu akuti, “Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
ולרשע אמר אלהים מה-לך לספר חקי ותשא בריתי עלי-פיך
17 Iwe umadana ndi malangizo anga ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
ואתה שנאת מוסר ותשלך דברי אחריך
18 Ukaona wakuba umamutsatira, umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
אם-ראית גנב ותרץ עמו ועם מנאפים חלקך
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
פיך שלחת ברעה ולשונך תצמיד מרמה
20 Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
תשב באחיך תדבר בבן-אמך תתן-דפי
21 Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete; umaganiza kuti ndine wofanana nawe koma ndidzakudzudzula ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
אלה עשית והחרשתי-- דמית היות-אהיה כמוך אוכיחך ואערכה לעיניך
22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
בינו-נא זאת שכחי אלוה פן-אטרף ואין מציל
23 Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza, ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse chipulumutso cha Mulungu.”
זבח תודה יכבדנני ושם דרך--אראנו בישע אלהים

< Masalimo 50 >