< Masalimo 40 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga. 2 Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko, mʼthope ndi mʼchithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba. 3 Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga, nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga. Ambiri adzaona, nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova. 4 Ndi wodala munthu amakhulupirira Yehova; amene sayembekezera kwa odzikuza, kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza. 5 Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza. 6 Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna, koma makutu anga mwawatsekula; zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo Inu simunazipemphe. 7 Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera. Mʼbuku mwalembedwa za ine. 8 Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga; lamulo lanu lili mu mtima mwanga.” 9 Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova. 10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu. 11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova; chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse. 12 Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira; machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona. Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga, ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga. 13 Pulumutseni Yehova; Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza. 14 Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene amakhumba chiwonongeko changa abwezedwe mwamanyazi. 15 Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!” abwerere akuchita manyazi. 16 Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!” 17 Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.

< Masalimo 40 >