< Masalimo 39 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide. Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe; ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.” 2 Koma pamene ndinali chete osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino mavuto anga anachulukirabe. 3 Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga, ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka; kenaka ndinayankhula ndi lilime langa: 4 “Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga ndi chiwerengero cha masiku anga; mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani. 5 Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri, kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu; moyo wa munthu aliyense ndi waufupi. (Sela) 6 Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku: Iye amangovutika koma popanda phindu; amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani. 7 “Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani? Chiyembekezo changa chili mwa Inu. 8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse; musandisandutse chonyozeka kwa opusa. 9 Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi. 10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine; ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu. 11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo; mumawononga chuma chawo monga njenjete; munthu aliyense ali ngati mpweya. (Sela) 12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova, mverani kulira kwanga kopempha thandizo; musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu, popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa; monga anachitira makolo anga onse. 13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala ndisanafe ndi kuyiwalika.”

< Masalimo 39 >