< Masalimo 32 >

1 Salimo la Davide. Malangizo. Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa. 2 Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo. 3 Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse. 4 Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. (Sela) 5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” (Sela) 6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo pomwe mukupezeka; ndithu pamene madzi amphamvu auka, sadzamupeza. 7 Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. (Sela) 8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. 9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe. 10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye. 11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!

< Masalimo 32 >