< Masalimo 3 >

1 Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira! 2 Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” (Sela) 3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. 4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. (Sela) 5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza. 6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse. 7 Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa. 8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. (Sela)

< Masalimo 3 >