< Masalimo 24 >

1 Salimo la Davide. Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo; 2 pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi. 3 Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika? 4 Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo. 5 Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu. 6 Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova; amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo. (Sela) 7 Tukulani mitu yanu inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe. 8 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo. 9 Tukulani mitu yanu, inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe. 10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Iye ndiye Mfumu yaulemerero. (Sela)

< Masalimo 24 >