< Masalimo 21 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu, chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
לַמְנַצֵּ֗חַ מִזְמֹ֥ור לְדָוִֽד׃ יְֽהוָ֗ה בְּעָזְּךָ֥ יִשְׂמַח־מֶ֑לֶךְ וּ֝בִישׁ֥וּעָתְךָ֗ מַה־יָּ֥גֶיל מְאֹֽד׃
2 Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake. (Sela)
תַּאֲוַ֣ת לִ֭בֹּו נָתַ֣תָּה לֹּ֑ו וַאֲרֶ֥שֶׁת שְׂ֝פָתָ֗יו בַּל־מָנַ֥עְתָּ סֶּֽלָה׃
3 Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
כִּֽי־תְ֭קַדְּמֶנּוּ בִּרְכֹ֣ות טֹ֑וב תָּשִׁ֥ית לְ֝רֹאשֹׁ֗ו עֲטֶ֣רֶת פָּֽז׃
4 Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa masiku ochuluka kwamuyaya.
חַיִּ֤ים ׀ שָׁאַ֣ל מִ֭מְּךָ נָתַ֣תָּה לֹּ֑ו אֹ֥רֶךְ יָ֝מִ֗ים עֹולָ֥ם וָעֶֽד׃
5 Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
גָּדֹ֣ול כְּ֭בֹודֹו בִּישׁוּעָתֶ֑ךָ הֹ֥וד וְ֝הָדָר תְּשַׁוֶּ֥ה עָלָֽיו׃
6 Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya, Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
כִּֽי־תְשִׁיתֵ֣הוּ בְרָכֹ֣ות לָעַ֑ד תְּחַדֵּ֥הוּ בְ֝שִׂמְחָ֗ה אֶת־פָּנֶֽיךָ׃
7 Pakuti mfumu imadalira Yehova; kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba, iyo sidzagwedezeka.
כִּֽי־הַ֭מֶּלֶךְ בֹּטֵ֣חַ בַּיהוָ֑ה וּבְחֶ֥סֶד עֶ֝לְיֹ֗ון בַּל־יִמֹּֽוט׃
8 Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse; dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
תִּמְצָ֣א יָ֭דְךָ לְכָל־אֹיְבֶ֑יךָ יְ֝מִֽינְךָ תִּמְצָ֥א שֹׂנְאֶֽיךָ׃
9 Pa nthawi ya kuonekera kwanu mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha. Mu ukali wake Yehova adzawameza, ndipo moto wake udzawatha.
תְּשִׁיתֵ֤מֹו ׀ כְּתַנּ֥וּר אֵשׁ֮ לְעֵ֪ת פָּ֫נֶ֥יךָ יְ֭הוָה בְּאַפֹּ֣ו יְבַלְּעֵ֑ם וְֽתֹאכְלֵ֥ם אֵֽשׁ׃
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi, zidzukulu zawo pakati pa anthu.
פִּ֭רְיָמֹו מֵאֶ֣רֶץ תְּאַבֵּ֑ד וְ֝זַרְעָ֗ם מִבְּנֵ֥י אָדָֽם׃
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo sadzapambana;
כִּי־נָט֣וּ עָלֶ֣יךָ רָעָ֑ה חָֽשְׁב֥וּ מְ֝זִמָּ֗ה בַּל־יוּכָֽלוּ׃
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.
כִּ֭י תְּשִׁיתֵ֣מֹו שֶׁ֑כֶם בְּ֝מֵֽיתָרֶ֗יךָ תְּכֹונֵ֥ן עַל־פְּנֵיהֶֽם׃
13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu, ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.
ר֣וּמָה יְהוָ֣ה בְעֻזֶּ֑ךָ נָשִׁ֥ירָה וּֽ֝נְזַמְּרָה גְּבוּרָתֶֽךָ׃

< Masalimo 21 >