< Masalimo 16 >

1 Mikitamu ya Davide. Ndisungeni Inu Mulungu, pakuti ine ndimathawira kwa Inu. 2 Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga; popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.” 3 Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko, amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo. 4 Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga. 5 Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa. 6 Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri. 7 Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza. 8 Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. 9 Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino, 10 chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde. (Sheol h7585) 11 Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

< Masalimo 16 >