< Masalimo 141 >

1 Salimo la Davide. Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu. 2 Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo. 3 Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga. 4 Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo. 5 Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa. 6 Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri, ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino. 7 Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza, ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.” (Sheol h7585) 8 Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa. 9 Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera. 10 Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere.

< Masalimo 141 >