< Masalimo 14 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; palibe amene amachita zabwino. 2 Yehova kumwamba wayangʼana pansi, kuyangʼana anthu onse kuti aone ngati alipo wina wanzeru, amene amafunafuna Mulungu. 3 Onse atembenukira kumbali, onse pamodzi asanduka oyipa; palibe amene amachita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe. 4 Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse? Akudya anthu anga ngati chakudya chawo ndipo satamanda Yehova? 5 Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu, pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama. 6 Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka, koma Yehova ndiye pothawirapo pawo. 7 Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

< Masalimo 14 >