< Masalimo 138 >

1 Salimo la Davide. Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.” 2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse. 3 Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima. 4 Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova, pamene amva mawu a pakamwa panu. 5 Iwo ayimbe za njira za Yehova, pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu. 6 Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali. 7 Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja. 8 Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine; chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha musasiye ntchito ya manja anu.

< Masalimo 138 >