< Masalimo 137 >

1 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira pamene tinakumbukira Ziyoni. 2 Kumeneko, pa mitengo ya misondozi tinapachika apangwe athu, 3 pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo. Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo; iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!” 4 Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova mʼdziko lachilendo? 5 Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liyiwale luso lake. 6 Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu, ngati sindiyesa iwe chimwemwe changa chachikulu. 7 Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!” 8 Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa, wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera pa zimene watichitira. 9 Amene adzagwira makanda ako ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.

< Masalimo 137 >