< Masalimo 129 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli; 2 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane. 3 Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali: 4 Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.” 5 Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi. 6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule; 7 sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo. 8 Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

< Masalimo 129 >