< Masalimo 126 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota. 2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.” 3 Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe. 4 Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova, monga mitsinje ya ku Negevi. 5 Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe. 6 Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.

< Masalimo 126 >