< Masalimo 124 >

1 Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli,
大衛上行之詩。 以色列人要說: 若不是耶和華幫助我們,
2 akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo,
若不是耶和華幫助我們, 當人起來攻擊我們、
3 iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo;
向我們發怒的時候, 就把我們活活地吞了。
4 chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola,
那時,波濤必漫過我們, 河水必淹沒我們,
5 madzi a mkokomo akanatikokolola.
狂傲的水必淹沒我們。
6 Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
耶和華是應當稱頌的! 他沒有把我們當野食交給他們吞吃。
7 Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka.
我們好像雀鳥,從捕鳥人的網羅裏逃脫; 網羅破裂,我們逃脫了。
8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
我們得幫助, 是在乎倚靠造天地之耶和華的名。

< Masalimo 124 >