< Masalimo 123 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba. 2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo. 3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo, pakuti tapirira chitonzo chachikulu. 4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza, chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.

< Masalimo 123 >