< Masalimo 12 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide. Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu. 2 Aliyense amanamiza mʼbale wake; ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo. 3 Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo ndi pakamwa paliponse podzikuza. 4 Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu; pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?” 5 “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.” 6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri. 7 Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya. 8 Oyipa amangoyendayenda ponseponse anthu akamayamikira zochita zawo.

< Masalimo 12 >