< Masalimo 113 >

1 Tamandani Yehova. Mutamandeni, inu atumiki a Yehova, tamandani dzina la Yehova. 2 Yehova atamandidwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya. 3 Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake, dzina la Yehova liyenera kutamandidwa. 4 Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba. 5 Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu, Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba? 6 amene amawerama pansi kuyangʼana miyamba ndi dziko lapansi? 7 Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala; 8 amawakhazika pamodzi ndi mafumu, pamodzi ndi mafumu a anthu ake. 9 Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake monga mayi wa ana wosangalala. Tamandani Yehova.

< Masalimo 113 >