< Masalimo 111 >

1 Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano. 2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira. 3 Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha. 4 Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo. 5 Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya. 6 Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina. 7 Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika. 8 Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama. 9 Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa. 10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

< Masalimo 111 >