< Masalimo 11 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame. 2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima. 3 Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?” 4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa. 5 Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa. 6 Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera. 7 Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

< Masalimo 11 >