< Miyambo 8 >

1 Kodi nzeru sikuyitana? Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake? 2 Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira, imayima pa mphambano ya misewu. 3 Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda, pa makomo olowera imafuwula kuti, 4 Inu anthu, ndikuyitana inu; ndikuyitanatu anthu onse. 5 Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera; inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu. 6 Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri; ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama. 7 Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa. 8 Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama; mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka. 9 Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona; kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza. 10 Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino. 11 Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru. 12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera. Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino. 13 Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga. 14 Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino; ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu. 15 Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira. Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama. 16 Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula. Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko. 17 Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza. 18 Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika. 19 Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri. 20 Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo. 21 Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma. 22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine. 23 Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe. 24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa. 25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale, 26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi. 27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama, 28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama, 29 pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi. 30 Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake. 31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.” 32 “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga. 33 Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru; musanyozere mawu anga. 34 Wodala munthu amene amandimvera, amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku, kudikirira pa chitseko changa. 35 Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo ndipo Yehova amamukomera mtima. 36 Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha; onse amene amandida amakonda imfa.”

< Miyambo 8 >