< Numeri 4 >

1 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni:
The LORD spoke to Moses and to Aaron, saying,
2 “Werengani Akohati omwe ndi gawo limodzi la Alevi monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo.
"Take a census of the sons of Kohath from among the sons of Levi, by their families, by their fathers' houses,
3 Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano.
from thirty years old and upward even until fifty years old, all who enter into the service, to do the work in the Tent of Meeting.
4 “Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri.
This is the service of the sons of Kohath in the Tent of Meeting, the most holy things.
5 Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni.
When the camp moves forward, Aaron shall go in, and his sons, and they shall take down the veil of the screen, and cover the ark of the Testimony with it,
6 Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.
and shall put a covering of sealskin on it, and shall spread over it a cloth all of blue, and shall put in its poles.
7 “Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse.
On the table of show bread they shall spread a blue cloth, and put on it the dishes, the spoons, the bowls, and the pitchers for pouring with them; and the continual bread shall be on it.
8 Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.
They shall spread on them a scarlet cloth, and cover the same with a covering of sealskin, and shall put in its poles.
9 “Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta.
They shall take a blue cloth, and cover the lampstand of the light, and its lamps, and its snuffers, and its snuff dishes, and all its oil vessels, with which they minister to it.
10 Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake.
They shall put it and all its vessels within a covering of sealskin, and shall put it on the frame.
11 “Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.
On the golden altar they shall spread a blue cloth, and cover it with a covering of sealskin, and shall put in its poles.
12 “Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake.
They shall take all the vessels of ministry, with which they minister in the sanctuary, and put them in a blue cloth, and cover them with a covering of sealskin, and shall put them on the frame.
13 “Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake.
They shall take away the ashes from the altar, and spread a purple cloth on it.
14 Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake.
They shall put on it all its vessels, with which they minister about it, the fire pans, the flesh hooks, the shovels, and the basins; all the vessels of the altar; and they shall spread on it a covering of sealskin, and put in its poles.
15 “Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.
"When Aaron and his sons have finished covering the sanctuary, and all the furniture of the sanctuary, as the camp moves forward; after that, the sons of Kohath shall come to carry it: but they shall not touch the sanctuary, lest they die. These things are the burden of the sons of Kohath in the Tent of Meeting.
16 “Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.”
"The duty of Eleazar the son of Aaron the priest shall be the oil for the light, the sweet incense, the continual meal offering, and the anointing oil, the requirements of all the tabernacle, and of all that is in it, the sanctuary, and its furnishings."
17 Yehova anawuzanso Mose ndi Aaroni kuti,
The LORD spoke to Moses and to Aaron, saying,
18 “Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi.
"Do not cut off the tribe of the families of the Kohathites from among the Levites;
19 Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula.
but thus do to them, that they may live, and not die, when they approach to the most holy things: Aaron and his sons shall go in, and appoint them everyone to his service and to his burden;
20 Koma Akohati asalowe kukaona zinthu zopatulika, ngakhale kanthawi pangʼono, chifukwa akatero adzafa.”
but they shall not go in to see the sanctuary even for a moment, lest they die."
21 Yehova anawuza Mose kuti,
The LORD spoke to Moses, saying,
22 “Werenganso Ageresoni monga mwa mabanja ndi mafuko awo.
"Take a census of the sons of Gershon also, by their fathers' houses, by their families;
23 Uwerenge amuna onse a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu zakubadwa amene amabwera kudzatumikira ku tenti ya msonkhano.
you shall count them from thirty years old and upward until fifty years old; all who enter in to wait on the service, to do the work in the Tent of Meeting.
24 “Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi:
This is the service of the families of the Gershonites, in serving and in bearing burdens:
25 Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano,
they shall carry the curtains of the tabernacle, and the Tent of Meeting, its covering, and the covering of sealskin that is above on it, and the screen for the door of the Tent of Meeting,
26 makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi.
and the tapestries of the court, and the screen for the door of the gate of the court, which is by the tabernacle and around the altar, and their cords, and all the instruments of their service, and whatever shall be done with them. So they are to serve.
27 Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira.
At the commandment of Aaron and his sons shall be all the service of the sons of the Gershonites, in all their burden, and in all their service; and you shall appoint their duty to them in all their responsibilities.
28 Iyi ndiye ntchito ya fuko la Ageresoni ku tenti ya msonkhano. Ntchito zawo zichitike motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.
This is the service of the families of the sons of the Gershonites in the Tent of Meeting: and their duty shall be under the hand of Ithamar the son of Aaron the priest.
29 “Werenga Amerari monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo.
"As for the sons of Merari, you shall number them by their families, by their fathers' houses;
30 Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano.
you shall count them from thirty years old and upward even to fifty years old, everyone who enters on the service, to do the work of the Tent of Meeting.
31 Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde,
This is the duty of their burden, according to all their service in the Tent of Meeting: the tabernacle's boards, its bars, its pillars, its sockets,
32 ndiponso mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema, zingwe ndi zipangizo zake zonse ndiponso zonse zokhudzana ndi ntchito yake. Uwuze munthu aliyense chomwe ayenera kuchita.
and the pillars of the court around it, and their sockets, and their pins, and their cords, with all their instruments, and with all their service: and by name you shall appoint the instruments of the duty of their burden.
33 Iyi ndiyo ntchito ya mafuko a Amerari pamene akugwira ntchito ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.”
This is the service of the families of the sons of Merari, according to all their service, in the Tent of Meeting, under the hand of Ithamar the son of Aaron the priest."
34 Mose, Aaroni ndi atsogoleri a magulu a anthu anawerenga Akohati monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
Moses and Aaron and the leaders of the congregation numbered the sons of the Kohathites by their families, and by their fathers' houses,
35 Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano,
from thirty years old and upward even to fifty years old, everyone who entered into the service, for work in the Tent of Meeting.
36 atawawerenga mwa mafuko awo, anali 2,750.
Those who were numbered of them by their families were two thousand seven hundred fifty.
37 Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.
These are those who were numbered of the families of the Kohathites, all who served in the Tent of Meeting, whom Moses and Aaron numbered according to the commandment of the LORD by Moses.
38 Ageresoni anawerengedwanso monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
Those who were numbered of the sons of Gershon, their families, and by their fathers' houses,
39 Amuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano,
from thirty years old and upward even to fifty years old, everyone who entered into the service, for work in the Tent of Meeting,
40 atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630.
even those who were numbered of them, by their families, by their fathers' houses, were two thousand six hundred thirty.
41 Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.
These are those who were numbered of the families of the sons of Gershon, all who served in the Tent of Meeting, whom Moses and Aaron numbered according to the commandment of the LORD.
42 Amerari anawawerenga monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
Those who were numbered of the families of the sons of Merari, by their families, by their fathers' houses,
43 Amuna onse kuyambira zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzatumikira ntchito mu tenti ya msonkhano,
from thirty years old and upward even to fifty years old, everyone who entered into the service, for work in the Tent of Meeting,
44 atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 3,200.
even those who were numbered of them by their families, were three thousand two hundred.
45 Ichi ndicho chinali chiwerengero cha mabanja a Amerari. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga momwe Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose.
These are those who were numbered of the families of the sons of Merari, whom Moses and Aaron numbered according to the commandment of the LORD by Moses.
46 Kotero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a Israeli anawerenga Alevi onse monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
All those who were numbered of the Levites, whom Moses and Aaron and the leaders of Israel numbered, by their families, and by their fathers' houses,
47 Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu omwe anabwera kudzagwira ntchito yonyamula zinthu ku tenti ya msonkhano
from thirty years old and upward even to fifty years old, everyone who entered in to do the work of service, and the work of bearing burdens in the Tent of Meeting,
48 analipo 8,580.
even those who were numbered of them, were eight thousand five hundred eighty.
49 Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose.
According to the commandment of the LORD they were numbered by Moses, everyone according to his service, and according to his burden. Thus were they numbered by him, as the LORD commanded Moses.

< Numeri 4 >