< Numeri 10 >

1 Yehova anawuza Mose kuti,
L’Éternel parla à Moïse, et dit:
2 “Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa.
Fais-toi deux trompettes d’argent; tu les feras d’argent battu. Elles te serviront pour la convocation de l’assemblée et pour le départ des camps.
3 Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano.
Quand on en sonnera, toute l’assemblée se réunira auprès de toi, à l’entrée de la tente d’assignation.
4 Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe.
Si l’on ne sonne que d’une trompette, les princes, les chefs des milliers d’Israël, se réuniront auprès de toi.
5 Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka.
Quand vous sonnerez avec éclat, ceux qui campent à l’orient partiront;
6 Akaliza lipenga lochenjeza lachiwiri, misasa yakummwera iyambe kusamuka. Kuliza kwa lipenga lochenjeza kudzakhala chizindikiro choyamba ulendo.
quand vous sonnerez avec éclat pour la seconde fois, ceux qui campent au midi partiront: on sonnera avec éclat pour leur départ.
7 Pofuna kusonkhanitsa anthu, muziliza malipenga, koma mosiyana ndi mmene malipenga ochenjeza amalizidwira.
Vous sonnerez aussi pour convoquer l’assemblée, mais vous ne sonnerez pas avec éclat.
8 “Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse.
Les fils d’Aaron, les sacrificateurs, sonneront des trompettes. Ce sera une loi perpétuelle pour vous et pour vos descendants.
9 Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu.
Lorsque, dans votre pays, vous irez à la guerre contre l’ennemi qui vous combattra, vous sonnerez des trompettes avec éclat, et vous serez présents au souvenir de l’Éternel, votre Dieu, et vous serez délivrés de vos ennemis.
10 Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”
Dans vos jours de joie, dans vos fêtes, et à vos nouvelles lunes, vous sonnerez des trompettes, en offrant vos holocaustes et vos sacrifices d’actions de grâces, et elles vous mettront en souvenir devant votre Dieu. Je suis l’Éternel, votre Dieu.
11 Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni.
Le vingtième jour du second mois de la seconde année, la nuée s’éleva de dessus le tabernacle du témoignage.
12 Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani.
Et les enfants d’Israël partirent du désert de Sinaï, selon l’ordre fixé pour leur marche. La nuée s’arrêta dans le désert de Paran.
13 Kameneka kanali koyamba kuti Aisraeli anyamuke monga momwe Yehova analamulira Mose.
Ils firent ce premier départ sur l’ordre de l’Éternel par Moïse.
14 Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu.
La bannière du camp des fils de Juda partit la première, avec ses corps d’armée. Le corps d’armée de Juda était commandé par Nachschon, fils d’Amminadab;
15 Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanieli mwana wa Zuwara,
le corps d’armée de la tribu des fils d’Issacar, par Nethaneel, fils de Tsuar;
16 Eliabu mwana wa Heloni ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Zebuloni.
le corps d’armée de la tribu des fils de Zabulon, par Éliab, fils de Hélon.
17 Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka.
Le tabernacle fut démonté; et les fils de Guerschon et les fils de Merari partirent, portant le tabernacle.
18 Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri.
La bannière du camp de Ruben partit, avec ses corps d’armée. Le corps d’armée de Ruben était commandé par Élitsur, fils de Schedéur;
19 Mtsogoleri wa fuko la Simeoni anali Selumieli mwana wa Zurisadai,
le corps d’armée de la tribu des fils de Siméon, par Schelumiel, fils de Tsurischaddaï;
20 ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi.
le corps d’armée de la tribu des fils de Gad, par Éliasaph, fils de Déuel.
21 Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike.
Les Kehathites partirent, portant le sanctuaire; et l’on dressait le tabernacle en attendant leur arrivée.
22 Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo.
La bannière du camp des fils d’Éphraïm partit, avec ses corps d’armée. Le corps d’armée d’Éphraïm était commandé par Élischama, fils d’Ammihud;
23 Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase.
le corps d’armée de la tribu des fils de Manassé, par Gamliel, fils de Pedahtsur;
24 Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini.
le corps d’armée de la tribu des fils de Benjamin, par Abidan, fils de Guideoni.
25 Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
La bannière du camp des fils de Dan partit, avec ses corps d’armée: elle formait l’arrière-garde de tous les camps. Le corps d’armée de Dan était commandé par Ahiézer, fils d’Ammischaddaï;
26 Pagieli mwana wa Okirani ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Aseri,
le corps d’armée de la tribu des fils d’Aser, par Paguiel, fils d’Ocran;
27 ndipo mtsogoleri wa mtundu wa Nafutali anali Ahira mwana wa Enani.
le corps d’armée de la tribu des fils de Nephthali, par Ahira, fils d’Énan.
28 Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu.
Tel fut l’ordre d’après lequel les enfants d’Israël se mirent en marche selon leurs corps d’armée; et c’est ainsi qu’ils partirent.
29 Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”
Moïse dit à Hobab, fils de Réuel, le Madianite, beau-père de Moïse: Nous partons pour le lieu dont l’Éternel a dit: Je vous le donnerai. Viens avec nous, et nous te ferons du bien, car l’Éternel a promis de faire du bien à Israël.
30 Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.”
Hobab lui répondit: Je n’irai point; mais j’irai dans mon pays et dans ma patrie.
31 Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu.
Et Moïse dit: Ne nous quitte pas, je te prie; puisque tu connais les lieux où nous campons dans le désert, tu nous serviras de guide.
32 Iweyo ukapita nafe, tidzagawana nawe zinthu zabwino zomwe Yehova adzatipatsa.”
Et si tu viens avec nous, nous te ferons jouir du bien que l’Éternel nous fera.
33 Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo.
Ils partirent de la montagne de l’Éternel, et marchèrent trois jours; l’arche de l’alliance de l’Éternel partit devant eux, et fit une marche de trois jours, pour leur chercher un lieu de repos.
34 Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo.
La nuée de l’Éternel était au-dessus d’eux pendant le jour, lorsqu’ils partaient du camp.
35 Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, “Dzukani, Inu Yehova! Adani anu abalalike; Odana nanu athawe pamaso panu.
Quand l’arche partait, Moïse disait: Lève-toi, Éternel! Et que tes ennemis soient dispersés! Que ceux qui te haïssent fuient devant ta face!
36 “Pamene likupumula, ankanena kuti, “Bwererani, Inu Yehova, ku chinamtindi cha Aisraeli.”
Et quand on la posait, il disait: Reviens, Éternel, aux myriades des milliers d’Israël!

< Numeri 10 >