< Nehemiya 13 >

1 Pa tsiku limenelo anawerenga buku la Mose anthu akumva. Ndipo anapeza mawu akuti, Mwamoni kapena Mmowabu asalowe konse mu msonkhano wa Mulungu.
In that day they read in the book of Moses in the ears of the people; and it was found written in it, that the Ammonites and Moabites should not enter into the congregation of God for ever;
2 Paja iwowa sanawachingamire Aisraeli kukawapatsa chakudya ndi madzi. Mʼmalo mwake analemba ganyu Baalamu kuti adzawatemberere. Komabe Mulungu wathu anasandutsa tembererolo kukhala mdalitso.
because they met not the children of Israel with bread and water, but hired Balaam against them to curse them: but our God turned the curse into a blessing.
3 Anthu atamva lamuloli, anachotsa pakati pawo onse amene anali achilendo.
And it came to pass, when they heard the law, that they were separated, [even] every alien in Israel.
4 Izi zisanachitike, wansembe Eliyasibu anali atasankhidwa kukhala woyangʼanira zipinda zosungiramo katundu za Nyumba ya Mulungu. Iyeyu ankagwirizana kwambiri ndi Tobiya.
And before this time Eliasib the priest dwelt in the treasury of the house of our God, connected with Tobias;
5 Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe.
and he made himself a great treasury, and there they were formerly in the habit of bestowing the offerings, and the frankincense, and the vessels, and the tithe of the corn, and the wine, and the oil, the ordered portion of the Levites, and singers, and porters; and the first-fruits of the priests.
6 Koma pamene izi zonse zinkachitika mu Yerusalemu, ine kunalibe popeza mʼchaka cha 32 cha Aritasasita mfumu ya Babuloni ine ndinabwerera kwa mfumu. Patapitanso nthawi ndinapempha chilolezo kwa mfumuyo
But in all this [time] I was not in Jerusalem; for in the thirty-second year of Arthasastha king of Babylon I came to the king, and after a certain time I made my request of the king;
7 ndipo ndinabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko ndinamva za chinthu choyipa chimene Eliyasibu anachita pomupatsa Tobiya chipinda mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.
and I came to Jerusalem, and I understood the mischief which Eliasib had done in the case of Tobias, in making for him a treasury in the court of the house of God.
8 Ndinapsa mtima kwambiri ndipo ndinataya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali mʼchipindamo.
And it appeared very evil to me: so I cast forth all the furniture of the house of Tobias from the treasury.
9 Ndinalamulira kuti ayeretse zipinda, ndipo kenaka ndinabwezeramo zida za mʼNyumba ya Mulungu, pamodzi ndi chopereka cha zakudya ndi lubani.
And I gave orders, and they purified the treasuries: and I restored thither the vessels of the house of God, [and] the offerings, and the frankincense.
10 Ndinapezanso kuti Alevi sankalandira magawo awo amene amayera kulandira. Chotsatira chake Alevi onse pamodzi ndi oyimba nyimbo amene ankagwira ku Nyumba ya Mulungu anathawa, aliyense kupita ku munda wake.
And I understood that the portion of the Levites had not been given: and they had fled every one to his field, the Levites and the singers doing the work.
11 Choncho ndinadzudzula akuluakulu aja ndipo ndinawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa?” Ndipo ine ndinawayitanitsa pamodzi ndi kuwayika mʼmalo awo.
And I strove with the commanders, and said, Wherefore has the house of God been abandoned? and I assembled them, and set them in their place.
12 Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma.
And all Juda brought a tithe of the wheat and the wine and the oil into the treasuries,
13 Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika.
to the charge of Selemia the priest, and Sadoc the scribe, and Phadaea of the Levites: and next to them [was] Anan the son of Zacchur, son of Matthanias; for they were accounted faithful: [it was] their office to distribute to their brethren.
14 Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zimenezi, ndipo musafafanize ntchito zanga zimene ndachita mokhulupirika pa Nyumba yanu pofuna kukutumikirani.
Remember me, O God, in this, and let not my kindness be forgotten which I have wrought in [regard to] the house of the Lord God.
15 Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata.
In those days I saw in Juda [men] treading wine-presses on the sabbath, and carrying sheaves, and loading asses with both wine, and grapes, and figs, and every [kind of] burden, and bringing them into Jerusalem on the sabbath-day:
16 Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu.
and I testified in the day of their sale. Also their dwelt in it [men] bringing fish, and selling every [kind of] merchandise to the children of Juda and in Jerusalem on the sabbath.
17 Ndipo ndinadzudzula anthu olemekezeka a dziko la Yuda. Ndinawafunsa kuti, “Nʼchoyipa chanji mukuchitachi, kumayipitsa tsiku la Sabata chotere?
And I strove with the free children of Juda, and said to them, What [is] this evil thing which ye do, and profane the sabbath-day?
18 Makolo anu anachita zomwezi ndipo Mulungu wathu anadzetsa mavuto pa ife ndi pa mzinda uwu. Kodi inu mukufuna kuwutsanso mkwiyo wa Mulungu pa Israeli pamene mukudetsa tsiku la Sabata?”
Did not your fathers thus, and our God brought upon them and upon us and upon this city all these evils? and do ye bring additional wrath upon Israel by profaning the sabbath?
19 Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata.
And it came to pass, when the gates were set up in Jerusalem, before the sabbath, that I spoke, and they shut the gates; and I gave orders that they should not be opened till after the sabbath: and I set [some] of my servants at the gates, that none should bring [in] burdens on the sabbath-day.
20 Choncho kamodzi kapena kawiri anthu amalonda ndi anthu ogulitsa katundu osiyanasiyana ankagona usiku wonse kunja kwa Yerusalemu.
So all [the merchants] lodged, and carried on traffic without Jerusalem once or twice.
21 Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata.
Then I testified against them, and said to them, Why do ye lodge in front of the wall? if ye do so again, I will stretch out my hand upon you. From that time they came not on the sabbath.
22 Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera. Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
and I told the Levites who were purifying themselves, and came and kept the gates, that they should sanctify the sabbath-day. Remember me, O God, for these things, and spare me according to the abundance of thy mercy.
23 Masiku amenewo ndinaonanso anthu a ku Yuda amene anakwatira akazi ochokera ku Asidodi, Amoni ndi Mowabu.
And in those days I saw the Jews who had married women of Ashdod, of Ammon, [and] of Moab:
24 Theka la ana awo linkayankhula chiyankhulo cha Asidodi kapena chiyankhulo chimodzi cha anthu ena, ndipo sankathanso kuyankhula chiyankhulo cha Ayuda.
and their children spoke half in the language of Ashdod, and did not know how to speak in the Jewish language.
25 Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi.
And I strove with them and cursed them; and I smote some of them, and plucked off their hair, and made them swear by God, [saying, ]Ye shall not give your daughters to their sons, and ye shall not take of their daughters to your sons.
26 Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo.
Did not Solomon king of Israel sin thus? though there was no king like him among many nations, and he was beloved of God, and God made him king over all Israel; yet strange women turned him aside.
27 Kodi tsopano ife tizimva inu kuti mukuchita choyipa chachikulu chimenechi, kupandukira Yehova Mulungu wathu pomakwatira akazi achilendo?”
So we will not hearken to you to do all this evil, to break covenant with our God, —to marry strange wives.
28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga.
and Elisub the high priest, [one] of the sons of Joada, [being] son-in-law of Sanaballat the Uranite, I chased him away from me.
29 Inu Mulungu wanga, mukumbukire mmene iwo anayipitsira unsembe, pangano la unsembe komanso la Alevi.
Remember them, O God, for their [false] connection with the priesthood, and [the breaking] the covenant of the priesthood, and [for defiling] the Levites.
30 Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake.
So I purged them from all foreign connection, and established courses for the priests and the Levites, [every] man according to his work.
31 Ndiponso kupereka nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha pa nthawi yake. Ndikumbukireni pondikomera mtima, Inu Mulungu wanga.
And the offering of the wood-bearers [was] at certain set times, and in the [times of the] first-fruits. Remember me, O our God, for good.

< Nehemiya 13 >