< Yohane 17 >

1 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. 2 Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. (aiōnios g166) 3 Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. (aiōnios g166) 4 Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. 5 Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe. 6 “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7 Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8 Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9 Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe. 13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14 Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16 Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18 Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19 Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni. 20 “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21 Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22 Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23 Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine. 24 “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe. 25 “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26 Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

< Yohane 17 >