< Yobu 14 >

1 “Munthu wobadwa mwa amayi amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.
“Man, who is born of a woman, is of few days, and full of trouble.
2 Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota; amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.
He grows up like a flower, and is cut down. He also flees like a shadow, and doesn’t continue.
3 Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa? Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?
Do you open your eyes on such a one, and bring me into judgment with you?
4 Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa? Palibe ndi mmodzi yemwe!
Who can bring a clean thing out of an unclean? Not one.
5 Masiku a munthu ndi odziwikiratu; munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.
Seeing his days are determined, the number of his months is with you, and you have appointed his bounds that he can’t pass.
6 Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.
Look away from him, that he may rest, until he accomplishes, as a hireling, his day.
7 “Mtengo uli nacho chiyembekezo: ngati wadulidwa, udzaphukiranso ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.
“For there is hope for a tree if it is cut down, that it will sprout again, that the tender branch of it will not cease.
8 Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,
Though its root grows old in the earth, and its stock dies in the ground,
9 koma pamene chinyontho chafika udzaphukira ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.
yet through the scent of water it will bud, and sprout boughs like a plant.
10 Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda, amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.
But man dies, and is laid low. Yes, man gives up the spirit, and where is he?
11 Monga madzi amaphwera mʼnyanja kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,
As the waters fail from the sea, and the river wastes and dries up,
12 momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso; mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka kapena kudzutsidwa ku tulo tawo.
so man lies down and doesn’t rise. Until the heavens are no more, they will not awake, nor be roused out of their sleep.
13 “Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita! Achikhala munandiyikira nthawi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. (Sheol h7585)
“Oh that you would hide me in Sheol, that you would keep me secret until your wrath is past, that you would appoint me a set time and remember me! (Sheol h7585)
14 Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo? Masiku anga onse a moyo wovutikawu ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.
If a man dies, will he live again? I would wait all the days of my warfare, until my release should come.
15 Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani; inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu.
You would call, and I would answer you. You would have a desire for the work of your hands.
16 Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga koma simudzalondola tchimo langa.
But now you count my steps. Don’t you watch over my sin?
17 Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba; inu mudzaphimba tchimo langa.
My disobedience is sealed up in a bag. You fasten up my iniquity.
18 “Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake,
“But the mountain falling comes to nothing. The rock is removed out of its place.
19 monganso madzi oyenda amaperesera miyala ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka, momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu.
The waters wear the stones. The torrents of it wash away the dust of the earth. So you destroy the hope of man.
20 Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu; Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali.
You forever prevail against him, and he departs. You change his face, and send him away.
21 Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo; akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo.
His sons come to honor, and he doesn’t know it. They are brought low, but he doesn’t perceive it of them.
22 Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”
But his flesh on him has pain, and his soul within him mourns.”

< Yobu 14 >