< Yobu 14 >

1 “Munthu wobadwa mwa amayi amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha. 2 Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota; amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa. 3 Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa? Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu? 4 Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa? Palibe ndi mmodzi yemwe! 5 Masiku a munthu ndi odziwikiratu; munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha. 6 Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu. 7 “Mtengo uli nacho chiyembekezo: ngati wadulidwa, udzaphukiranso ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira. 8 Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi, 9 koma pamene chinyontho chafika udzaphukira ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete. 10 Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda, amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko. 11 Monga madzi amaphwera mʼnyanja kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma, 12 momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso; mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka kapena kudzutsidwa ku tulo tawo. 13 “Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita! Achikhala munandiyikira nthawi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. (Sheol h7585) 14 Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo? Masiku anga onse a moyo wovutikawu ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa. 15 Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani; inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu. 16 Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga koma simudzalondola tchimo langa. 17 Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba; inu mudzaphimba tchimo langa. 18 “Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake, 19 monganso madzi oyenda amaperesera miyala ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka, momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu. 20 Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu; Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali. 21 Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo; akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo. 22 Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”

< Yobu 14 >