< Yeremiya 9 >

1 Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi, ndi maso anga ngati kasupe wa misozi! Ndikanalira usana ndi usiku kulirira anthu anga amene aphedwa.
Wer gäbe, daß mein Haupt Wasser werde, und mein Auge ein Born der Tränen, daß ich bei Tag und Nacht beweinete die Erschlagenen der Tochter meines Volkes!
2 Ndani adzandipatsa malo ogona mʼchipululu kuti ndiwasiye anthu anga ndi kuwachokera kupita kutali; pakuti onse ndi achigololo, ndiponso gulu la anthu onyenga.
Wer gibt Mir in der Wüste eine Herberge der Reisenden, so verließe Ich Mein Volk und ginge von ihnen; denn sie alle sind Ehebrecher, eine Rotte von Treulosen.
3 “Amapinda lilime lawo ngati uta. Mʼdzikomo mwadzaza ndi mabodza okhaokha osati zoonadi. Amapitirirabe kuchita zoyipa; ndipo sandidziwa Ine.” Akutero Yehova.
Und sie spannen ihre Zungen als ihren Bogen der Lüge, und nicht für Wahrheit sind mächtig sie im Lande; denn von Bösem gehen sie auf Böses aus, und Mich kennen sie nicht, spricht Jehovah.
4 “Aliyense achenjere ndi abwenzi ake; asadalire ngakhale abale ake. Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu. Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
Der Mann hüte sich vor seinem Genossen, und vertraue auf keinen Bruder; denn jeder Bruder überlistet und jeder Genosse geht als Zwischenträger um.
5 Aliyense amamunamiza mʼbale wake ndipo palibe amene amayankhula choonadi. Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza; amalimbika kuchita machimo.
Und der Mann hintergeht seinen Genossen, und Wahrheit reden sie nicht. Sie lehren ihre Zunge Lüge reden. Sie mühen sich ab, verkehrt zu handeln.
6 Iwe wakhalira mʼchinyengo ndipo ukukana kundidziwa Ine,” akutero Yehova.
Du wohnst mitten unter Trug. Vor Trug weigern sie sich, Mich zu erkennen, spricht Jehovah.
7 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa. Kodi ndingachite nawonso bwanji chifukwa cha machimo awo?
Darum spricht also Jehovah der Heerscharen: Siehe, läutern und prüfen will Ich sie. Denn was sollte Ich tun vor der Tochter Meines Volkes?
8 Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa; limayankhula zachinyengo. Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake, koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
Ein geschärfter Pfeil ist ihre Zunge. Trug redet sie. Mit seinem Munde redet er Frieden mit dem Genossen, und in seinem Inneren legt er ihm einen Hinterhalt.
9 Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi? akutero Yehova. ‘Kodi ndisawulipsire mtundu wotere wa anthu?’”
Sollte über solchem Ich sie nicht heimsuchen? spricht Jehovah. Sollte an einer Völkerschaft wie diese nicht Meine Seele Rache nehmen?
10 Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu. Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako, ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe. Mbalame zamlengalenga zathawa ndipo nyama zakuthengo zachokako.
Über die Berge will Ich ein Weinen erheben und ein Trauerlied, und über der Wüste Auen ein Klagelied. Denn sie sind versengt, so daß kein Mann vorübergeht, und man nicht hört die Stimme der Viehherde. Sie sind entflohen, hingegangen, vom Gevögel der Himmel bis zum Vieh.
11 Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja, malo okhalamo ankhandwe; ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”
Und Ich gebe Jerusalem dahin, zum Trümmerhaufen, zur Wohnstätte der Drachen und die Städte Jehudahs gebe Ich zur Verwüstung ohne Bewohner.
12 Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
Wer ist der weise Mann, daß er dies einsehe und zu dem Jehovahs Mund geredet, daß er es ansage? Weshalb wird dieses Land zerstört, versengt wie die Wüste, daß niemand durchgeht?
13 Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala.
Und Jehovah spricht: Darum, daß sie verlassen Mein Gesetz, das Ich vor sie gegeben, und auf Meine Stimme nicht gehört und nicht danach gewandelt haben;
14 Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.”
Und gingen der Verstocktheit ihrer Herzen nach und nach den Baalen, wie ihre Väter sie gelehrt hatten.
15 Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu.
Darum, so spricht Jehovah der Heerscharen, der Gott Israels, siehe, Ich lasse dieses Volk Wermut essen und tränke sie mit Wasser der Galle.
16 Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
Und zerstreue sie unter die Völkerschaften, die weder sie selbst noch ihre Väter kannten, und sende ihnen das Schwert nach, bis Ich sie aufgerieben.
17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere; itanani akazi odziwa kulira bwino.”
So spricht Jehovah der Heerscharen: Merket auf und ruft den Klageweibern, daß sie kommen, und sendet nach den weisen Frauen, daß sie kommen.
18 Anthu akuti, “Abwere mofulumira kuti adzatilire mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
Daß sie eilen und über uns das Trauerlied erheben, und Tränen von unseren Augen herabrinnen, und Wasser von unseren Wim- pern riesle.
19 Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti, ‘Aa! Ife tawonongeka! Tachita manyazi kwambiri! Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’”
Denn aus Zijon hört man des Trauerliedes Stimme: Wie sind wir verheert, wir sind beschämt sehr. Denn wir verlassen das Land, denn niedergeworfen sind unsere Wohnungen.
20 Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova; tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova. Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni; aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
Ja, höret, ihr Weiber, Jehovahs Wort, und Seines Mundes Wort nehmet zu Ohr, und lehret eure Töchter das Trauerlied und das Weib die Genossin das Klagelied.
21 Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa; yapha ana athu mʼmisewu, ndi achinyamata athu mʼmabwalo.
Denn zu unseren Fenstern steigt herauf der Tod, er kommt in unsere Paläste, auszurotten das Kindlein aus der Gasse, die Jünglinge aus der Straße.
22 Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti, “‘Mitembo ya anthu idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda, ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola, popanda munthu woyitola.’”
Rede: So spricht Jehovah: Wie Dünger fällt des Menschen Leichnam auf des Feldes Angesicht und wie die Garbe hinter dem Schnitter, und keiner sammelt sie.
23 Yehova akuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake, kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
So spricht Jehovah: Nicht rühme der Weise sich seiner Weisheit und nicht rühme der Mächtige sich seiner Macht; nicht rühme der Reiche sich seines Reichtums.
24 koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi: kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa, kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo, chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi. Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,” akutero Yehova.
Sondern wer sich rühmen will, der rühme sich, daß er verständig ist und Mich kennt, daß Ich Jehovah bin, Welcher tut Barmherzigkeit, Recht und Gerechtigkeit auf Erden; denn daran habe Ich Lust, spricht Jehovah.
25 “Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe.
Siehe, es kommen Tage, spricht Jehovah, daß Ich an allen die Beschneidung in der Vorhaut heimsuche.
26 Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”
An Ägypten und an Jehudah und an Edom, und an den Söhnen Ammons und an Moab und an allen, welche die Ecke stutzen, die in der Wüste wohnen; denn alle die Heiden sind unbeschnitten und das ganze Haus Israels ist unbeschnittenen Herzens.

< Yeremiya 9 >