< Yeremiya 47 >

1 Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu: 2 Yehova akuti, “Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto; adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo. Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo, mizinda ndi onse okhala mʼmenemo. Anthu adzafuwula; anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira 3 akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga, phokoso la magaleta ake ndi kulira kwa mikombero yake. Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo; manja awo adzangoti khoba. 4 Pakuti tsiku lafika lowononga Afilisti onse ndi kupha onse otsala, onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni. Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti, otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori. 5 Anthu a ku Gaza ameta mipala; anthu a ku Asikeloni akhala chete. Inu otsala a ku chigwa, mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti? 6 “Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova, kodi udzapumula liti? Bwerera mʼmalo ako; ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’ 7 Koma lupangalo lidzapumula bwanji pamene Yehova walilamulira kuti lithire nkhondo Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”

< Yeremiya 47 >