< Yeremiya 24 >

1 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova. 2 Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya. 3 Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.” 4 Tsono Yehova anandiwuza kuti, 5 “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi. 6 Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula. 7 Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse. 8 “‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto. 9 Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira. 10 Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’”

< Yeremiya 24 >