< Yeremiya 23 >

1 “Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova.
Woe to the shepherds that destroy and scatter the sheep of their pasture!
2 Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova.
Therefore thus saith the Lord against them that tend my people; Ye have scattered my sheep, and driven them out, and ye have not visited them: behold, I [will] take vengeance upon you according to your evil practices.
3 “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana.
And I will gather in the remnant of my people in every land, whither I have driven them out, and will set them in their pasture; and they shall increase and be multiplied.
4 Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
And I will raise up shepherds to them, who shall feed them: and they shall fear no more, nor be alarmed, saith the Lord.
5 Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
Behold, the days come, saith the Lord, when I will raise up to David a righteous branch, and a king shall reign and understand, and shall execute judgment and righteousness on the earth.
6 Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka ndipo Israeli adzakhala pamtendere. Dzina limene adzamutcha ndi ili: Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
In his days both Juda shall be saved, and Israel shall dwell securely: and this is his name, which the Lord shall call him, Josedec among the prophets.
7 Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’
Therefore, behold, the days come, saith the Lord, when they shall no more say, The Lord lives, who brought up the house of Israel out of the land of Egypt;
8 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
but The Lord lives, who has gathered the whole seed of Israel from the north land, and from all the countries whither he [had] driven them out, and has restored them into their own land.
9 Kunena za aneneri awa: Mtima wanga wasweka; mʼnkhongono mwati zii. Ndakhala ngati munthu woledzera, ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Yehova ndi mawu ake opatulika.
My heart is broken within me; all my bones are shaken: I am become as a broken-down man, and as a man overcome with wine, because of the Lord, and because of the excellence of his glory.
10 Dziko ladzaza ndi anthu achigololo; lili pansi pa matemberero. Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma. Aneneri akuchita zoyipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
For because of these things the land mourns; the pastures of the wilderness are dried up; and their course is become evil, and so [also] their strength.
11 “Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova. Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,” akutero Yehova.
For priest and prophet are defiled; and I have seen their iniquities in my house.
12 “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera; adzawapirikitsira ku mdima ndipo adzagwera kumeneko. Adzaona zosaona mʼnthawi ya chilango chawo,” akutero Yehova.
Therefore let their way be to them slippery and dark: and they shall be tripped up and fall in it: for I will bring evils upon them, in the year of their visitation.
13 “Pakati pa aneneri a ku Samariya ndinaona chonyansa ichi: Ankanenera mʼdzina la Baala ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
And in the prophets of Samaria I have seen lawless deeds; they prophesied by Baal, and led my people Israel astray.
14 Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita chigololo, amanena bodza ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa. Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake. Kwa Ine anthu onsewa ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
Also in the prophets of Jerusalem I have seen horrible things: as they committed adultery, and walked in lies, and strengthened the hands of many, that they should not return each from his evil way: they are all become to me as Sodom, and the inhabitants thereof as Gomorrha.
15 Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawadyetsa zakudya zowawa ndi kuwamwetsa madzi a ndulu, chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
Therefore thus saith the Lord; Behold, I will feed them with pain, and give them bitter water to drink: for from the prophets of Jerusalem has defilement gone forth [into] all the land.
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu; zomwe aloserazo nʼzachabechabe. Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi, osati zochokera kwa Yehova.
Thus saith the Lord Almighty, Hearken not to the words of the prophets: for they frame a vain vision for themselves; they speak from their own heart, and not from the mouth of the Lord.
17 Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti, ‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti, ‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’”
They say to them that reject the word of the Lord, There shall be peace to you; and to all that walk after their own lusts, and to everyone that walks in the error of his heart, they have said, No evil shall come upon thee.
18 Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova? Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake? Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
For who has stood in the counsel of the Lord, and seen his word? who has hearkened, and heard?
19 Taonani ukali wa Yehova uli ngati chimphepo chamkuntho, inde ngati namondwe. Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
Behold, [there is] an earthquake from the Lord, and anger proceeds to a convulsion, it shall come violently upon the ungodly.
20 Mkwiyo wa Yehova sudzaleka mpaka atachita zonse zimene anatsimikiza mu mtima mwake. Mudzazizindikira bwino zimenezi masiku akubwerawa.”
And the Lord's wrath shall return no more, until he have accomplished it, and until he have established it, according to the purpose of his heart: at the end of the days they shall understand it.
21 Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa, komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo; Ine sindinawayankhule, komabe iwo ananenera.
I sent not the prophets, yet they ran: neither spoke I to them, yet they prophesied.
22 Iwo akanakhala pa msonkhano wanga ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga. Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa kuti aleke machimo awo.”
But if they had stood in my counsel, and if they had hearkened to my words, then would they have turned my people from their evil practices.
23 Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, ndiye sindine Mulungu?
I am a God nigh at hand, saith the Lord, and not a God afar off.
24 Kodi wina angathe kubisala Ine osamuona?” “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?” Akutero Yehova.
Shall any one hide himself in secret places, and I not see him? Do I not fill heaven and earth? saith the Lord.
25 “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’
I have heard what the prophets say, what they prophesy in my name, saying falsely, I have seen a night vision.
26 Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo.
How long shall [these things] be in the heart of the prophets that prophesy lies, when they prophesy the purposes of their own heart?
27 Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala.
who devise that [men] may forget my law by their dreams, which they have told every one to his neighbour, as their fathers forgot my name in [the worship of] Baal.
28 Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga?
The prophet who has a dream, let him tell his dream; and [he] in whom is my word [spoken] to him, let him tell my word truly: what is the chaff to the corn? so are my words, saith the Lord.
29 Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
Behold, are not my words as fire? saith the Lord; and as an axe cutting the rock?
30 Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.”
Behold, I am therefore against the prophets, saith the Lord God, that steal my words every one from his neighbour.
31 Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’”
Behold, I am against the prophets that put forth prophecies of mere words, and slumber their sleep.
32 Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Therefore, behold, I am against the prophets that prophesy false dreams, and have not told them [truly], and have caused my people to err by their lies, and by their errors; yet I sent them not, and commanded them not; therefore, they shall not profit this people at all.
33 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’
And if this people, or the priest, or the prophet, should ask, What is the burden of the Lord? then thou shalt say to them, Ye are the burden, and I will dash you down, saith the Lord.
34 Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake.
[As for] the prophet, and the priests, and the people, who shall say, The burden of the Lord, I will even take vengeance on that man, and on his house.
35 Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’
Thus shall ye say every one to his neighbour, and every one to his brother, What has the Lord answered? and, what has the Lord said?
36 Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
And do ye name no more the burden of the Lord; for his own word shall be a man's burden.
37 Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’
But wherefore, [say ye], has the Lord our God spoken?
38 Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule,
Therefore thus saith the Lord our God; Because ye have spoken this word, The burden of the Lord, and I sent to you, saying, ye shall not say, The burden of the Lord;
39 ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu.
therefore, behold, I [will] seize, and dash down you and the city which I gave to you and your fathers.
40 Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’”
And I will bring upon you an everlasting reproach, and everlasting disgrace, which shall not be forgotten.

< Yeremiya 23 >