< Yeremiya 14 >

1 Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:
耶和華論到乾旱之災的話臨到耶利米:
2 “Yuda akulira, mizinda yake ikuvutika; anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni, kulira kwa Yerusalemu kwakula.
猶大悲哀,城門衰敗。 眾人披上黑衣坐在地上; 耶路撒冷的哀聲上達。
3 Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi. Apita ku zitsime osapezako madzi. Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi. Amanyazi ndi othedwa nzeru adziphimba kumaso.
他們的貴冑打發家僮打水; 他們來到水池, 見沒有水,就拿着空器皿, 蒙羞慚愧,抱頭而回。
4 Popeza pansi pawumiratu chifukwa kulibe madzi, alimi ali ndi manyazi ndipo amphimba nkhope zawo.
耕地的也蒙羞抱頭; 因為無雨降在地上, 地都乾裂。
5 Ngakhale mbawala yayikazi ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo chifukwa kulibe msipu.
田野的母鹿生下小鹿,就撇棄, 因為無草。
6 Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe; maso awo achita chidima chifukwa chosowa msipu.”
野驢站在淨光的高處,喘氣好像野狗; 因為無草,眼目失明。
7 Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa, koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu. Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu; ife takuchimwirani.
耶和華啊,我們的罪孽雖然作見證告我們, 還求你為你名的緣故行事。 我們本是多次背道,得罪了你。
8 Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso, chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno? Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
以色列所盼望、在患難時作他救主的啊, 你為何在這地像寄居的, 又像行路的只住一宵呢?
9 Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa, kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa? Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu, ndipo tikudziwika ndi dzina lanu; musatitaye ife!”
你為何像受驚的人, 像不能救人的勇士呢? 耶和華啊,你仍在我們中間; 我們也稱為你名下的人, 求你不要離開我們。
10 Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi: “Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri; samatha kudziretsa. Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire, ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
耶和華對這百姓如此說: 這百姓喜愛妄行, 不禁止腳步, 所以耶和華不悅納他們。 現今要記念他們的罪孽, 追討他們的罪惡。
11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.
耶和華又對我說:「不要為這百姓祈禱求好處。
12 Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”
他們禁食的時候,我不聽他們的呼求;他們獻燔祭和素祭,我也不悅納;我卻要用刀劍、饑荒、瘟疫滅絕他們。」
13 Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”
我就說:「唉!主耶和華啊,那些先知常對他們說:『你們必不看見刀劍,也不遭遇饑荒;耶和華要在這地方賜你們長久的平安。』」
14 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo.
耶和華對我說:「那些先知託我的名說假預言,我並沒有打發他們,沒有吩咐他們,也沒有對他們說話;他們向你們預言的,乃是虛假的異象和占卜,並虛無的事,以及本心的詭詐。
15 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala.
所以耶和華如此說:論到託我名說預言的那些先知,我並沒有打發他們;他們還說這地不能有刀劍饑荒,其實那些先知必被刀劍饑荒滅絕。
16 Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.
聽他們說預言的百姓必因饑荒刀劍拋在耶路撒冷的街道上,無人葬埋。他們連妻子帶兒女,都是如此。我必將他們的惡倒在他們身上。」
17 “Awuze mawu awa: “‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza usana ndi usiku; chifukwa anthu anga okondedwa apwetekeka kwambiri, akanthidwa kwambiri.
你要將這話對他們說: 願我眼淚汪汪, 晝夜不息, 因為我百姓受了裂口破壞的大傷。
18 Ndikapita kuthengo, ndikuona amene aphedwa ndi lupanga; ndikapita mu mzinda, ndikuona amene asakazidwa ndi njala. Ngakhale aneneri pamodzi ndi ansembe onse atengedwa.’”
我若出往田間, 就見有被刀殺的; 我若進入城內, 就見有因饑荒患病的; 連先知帶祭司在國中往來, 也是毫無知識。
19 Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu? Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni? Chifukwa chiyani mwatikantha chotere kuti sitingathenso kuchira? Ife tinayembekezera mtendere koma palibe chabwino chomwe chabwera, tinayembekezera kuchira koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
你全然棄掉猶大嗎? 你心厭惡錫安嗎? 為何擊打我們,以致無法醫治呢? 我們指望平安,卻得不着好處; 指望痊癒,不料,受了驚惶。
20 Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu ndiponso kulakwa kwa makolo athu; ndithu ife tinakuchimwiranidi.
耶和華啊,我們承認自己的罪惡, 和我們列祖的罪孽, 因我們得罪了你。
21 Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe; musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero. Kumbukirani pangano lanu ndi ife ndipo musachiphwanye.
求你為你名的緣故, 不厭惡我們, 不辱沒你榮耀的寶座。 求你追念, 不要背了與我們所立的約。
22 Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina, kodi pali mulungu amene angagwetse mvula? Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu, popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu amene mukhoza kuchita zimenezi.
外邦人虛無的神中有能降雨的嗎? 天能自降甘霖嗎? 耶和華-我們的上帝啊, 能如此的不是你嗎? 所以,我們仍要等候你, 因為這一切都是你所造的。

< Yeremiya 14 >