< Yesaya 58 >

1 “Fuwula kwambiri, usaleke. Mawu ako amveke ngati lipenga. Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo; uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.
你要大聲喊叫,不可止息; 揚起聲來,好像吹角。 向我百姓說明他們的過犯; 向雅各家說明他們的罪惡。
2 Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine; amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna, kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake. Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.
他們天天尋求我, 樂意明白我的道, 好像行義的國民, 不離棄他們上帝的典章, 向我求問公義的判語, 喜悅親近上帝。
3 Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala kudya pamene Inu simukulabadirapo? Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa pamene Inu simunasamalepo?’” Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani, ndipo mumazunza antchito anu onse.
他們說:我們禁食,你為何不看見呢? 我們刻苦己心,你為何不理會呢? 看哪,你們禁食的日子仍求利益, 勒逼人為你們做苦工。
4 Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana, mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka. Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.
你們禁食,卻互相爭競, 以凶惡的拳頭打人。 你們今日禁食, 不得使你們的聲音聽聞於上。
5 Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo? Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko, tsiku lokondweretsa Yehova?
這樣禁食豈是我所揀選、 使人刻苦己心的日子嗎? 豈是叫人垂頭像葦子, 用麻布和爐灰鋪在他以下嗎? 你這可稱為禁食、為耶和華所悅納的日子嗎?
6 “Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna: Kumasula maunyolo ozunzizira anthu ndi kumasula zingwe za goli, kupereka ufulu kwa oponderezedwa ndi kuphwanya goli lililonse?
我所揀選的禁食不是要鬆開凶惡的繩, 解下軛上的索, 使被欺壓的得自由, 折斷一切的軛嗎?
7 Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu? Osowa ndi ongoyendayenda, kodi mwawapatsa malo ogona? Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?
不是要把你的餅分給飢餓的人, 將飄流的窮人接到你家中, 見赤身的給他衣服遮體, 顧恤自己的骨肉而不掩藏嗎?
8 Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha, ndipo mabala anu adzachira msangamsanga; chilungamo chanu chidzakutsogolerani ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.
這樣,你的光就必發現如早晨的光; 你所得的醫治要速速發明。 你的公義必在你前面行; 耶和華的榮光必作你的後盾。
9 Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani; mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano. “Ngati muleka kuzunza anzanu, ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.
那時你求告,耶和華必應允; 你呼求,他必說:我在這裏。 你若從你中間除掉重軛 和指摘人的指頭,並發惡言的事,
10 Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.
你心若向飢餓的人發憐憫, 使困苦的人得滿足, 你的光就必在黑暗中發現; 你的幽暗必變如正午。
11 Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse; adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa ndipo adzalimbitsa matupi anu. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe amene madzi ake saphwa.
耶和華也必時常引導你, 在乾旱之地使你心滿意足, 骨頭強壯。 你必像澆灌的園子, 又像水流不絕的泉源。
12 Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali, ndipo adzamanganso pa maziko akalekale; inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka. Anthu okonza misewu ndi nyumba zake.
那些出於你的人必修造久已荒廢之處; 你要建立拆毀累代的根基。 你必稱為補破口的, 和重修路徑與人居住的。
13 “Muzisunga osaphwanya Sabata; musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika, tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo. Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekeza posayenda mʼnjira zanu, kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake,
你若在安息日掉轉你的腳步, 在我聖日不以操作為喜樂, 稱安息日為可喜樂的, 稱耶和華的聖日為可尊重的; 而且尊敬這日, 不辦自己的私事, 不隨自己的私意, 不說自己的私話,
14 mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu.” Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.
你就以耶和華為樂。 耶和華要使你乘駕地的高處, 又以你祖雅各的產業養育你。 這是耶和華親口說的。

< Yesaya 58 >