< Yesaya 35 >

1 Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala; dziko lowuma lidzakondwa ndi kuchita maluwa. 2 Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu. 3 Limbitsani manja ofowoka, limbitsani mawondo agwedegwede; 4 nenani kwa a mitima yamantha kuti; “Limbani mtima, musachite mantha; Mulungu wanu akubwera, akubwera kudzalipsira; ndi kudzabwezera chilango adani anu; akubwera kudzakupulumutsani.” 5 Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka. 6 Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma, 7 mchenga wotentha udzasanduka dziwe, nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. Pamene panali mbuto ya ankhandwe padzamera udzu ndi bango. 8 Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo. 9 Kumeneko sikudzakhala mkango, ngakhale nyama yolusa sidzafikako; sidzapezeka konse kumeneko. Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu. 10 Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.

< Yesaya 35 >