< Yesaya 34 >

1 Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve: tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse: Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
קרבו גוים לשמע ולאמים הקשיבו תשמע הארץ ומלאה תבל וכל צאצאיה
2 Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse; wapsera mtima magulu awo onse ankhondo. Iye adzawawononga kotheratu, nawapereka kuti aphedwe.
כי קצף ליהוה על כל הגוים וחמה על כל צבאם החרימם נתנם לטבח
3 Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja, mitembo yawo idzawola ndi kununkha; mapiri adzafiira ndi magazi awo.
וחלליהם ישלכו ופגריהם יעלה באשם ונמסו הרים מדמם
4 Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala; nyenyezi zonse zidzayoyoka ngati masamba ofota a mphesa, ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
ונמקו כל צבא השמים ונגלו כספר השמים וכל צבאם יבול--כנבל עלה מגפן וכנבלת מתאנה
5 Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba; taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu, anthu amene ndawawononga kotheratu.”
כי רותה בשמים חרבי הנה על אדום תרד ועל עם חרמי למשפט
6 Lupanga la Yehova lakhuta magazi, lakutidwa ndi mafuta; magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi, mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna. Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
חרב ליהוה מלאה דם הדשנה מחלב מדם כרים ועתודים מחלב כליות אילים כי זבח ליהוה בבצרה וטבח גדול בארץ אדום
7 Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati, ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe. Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha, ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.
וירדו ראמים עמם ופרים עם אבירים ורותה ארצם מדם ועפרם מחלב ידשן
8 Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira ndi kulanga adani a Ziyoni.
כי יום נקם ליהוה--שנת שלומים לריב ציון
9 Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula, ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule; dziko lake lidzasanduka phula lamoto!
ונהפכו נחליה לזפת ועפרה לגפרית והיתה ארצה לזפת בערה
10 Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana; utsi wake udzafuka kosalekeza. Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado; palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.
לילה ויומם לא תכבה לעולם יעלה עשנה מדור לדור תחרב--לנצח נצחים אין עבר בה
11 Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu; amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo. Mulungu adzatambalitsa pa Edomu chingwe choyezera cha chisokonezo ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
וירשוה קאת וקפוד וינשוף וערב ישכנו בה ונטה עליה קו תהו ואבני בהו
12 Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko; akalonga ake onse adzachotsedwa.
חריה ואין שם מלוכה יקראו וכל שריה יהיו אפס
13 Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa, khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake. Ankhandwe azidzadya mʼmenemo; malo okhalamo akadzidzi.
ועלתה ארמנתיה סירים קמוש וחוח במבצריה והיתה נוה תנים חציר לבנות יענה
14 Avumbwe adzakumana ndi afisi, ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana. Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa ndi kupeza malo opumulirako.
ופגשו ציים את איים ושעיר על רעהו יקרא אך שם הרגיעה לילית ומצאה לה מנוח
15 Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira, adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake; akamtema adzasonkhananso kumeneko, awiriawiri.
שמה קננה קפוז ותמלט ובקעה ודגרה בצלה אך שם נקבצו דיות אשה רעותה
16 Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga: mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa; sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Yehova walamula kuti zitero, ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
דרשו מעל ספר יהוה וקראו--אחת מהנה לא נעדרה אשה רעותה לא פקדו כי פי הוא צוה ורוחו הוא קבצן
17 Yehova wagawa dziko lawo; wapatsa chilichonse chigawo chake. Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.
והוא הפיל להן גורל וידו חלקתה להם בקו עד עולם יירשוה--לדור ודור ישכנו בה

< Yesaya 34 >