< Hoseya 8 >

1 “Ika lipenga pakamwa pako. Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova chifukwa anthu aphwanya pangano langa ndiponso agalukira lamulo langa.
Set the trumpet to thy mouth. As an eagle he comes against the house of Jehovah, because they have transgressed my covenant, and trespassed against my law.
2 Israeli akulirira kwa Ine kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’
They shall cry to me, My God, we, Israel know thee.
3 Koma Israeli wakana zabwino; mdani adzamuthamangitsa.
Israel has cast off that which is good. The enemy shall pursue him.
4 Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amasankha akalonga popanda chilolezo changa. Amadzipangira mafano asiliva ndi agolide koma adzawonongeka nawo.
They have set up kings, but not by me. They have made rulers, and I knew it not. They have made themselves idols of their silver and their gold, that they may be cut off.
5 Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe! Mkwiyo wanga wayakira anthuwo. Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
He has cast off thy calf, O Samaria. My anger is kindled against them. How long will it be ere they attain to innocence?
6 Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya.
For even this is from Israel: the workman made it, and it is no God. Yea, the calf of Samaria shall be broken in pieces.
7 “Aisraeli amadzala mphepo ndipo amakolola kamvuluvulu. Tirigu alibe ngala; sadzabala chakudya. Akanabala chakudya alendo akanadya chakudyacho.
For they sow the wind, and they shall reap the whirlwind. He has no standing grain. The blade shall yield no meal. If so be it yields, strangers shall swallow it up.
8 Israeli wamezedwa, tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina ngati chinthu cha chabechabe.
Israel is swallowed up. They are now among the nations as a vessel in which no man delights.
9 Pakuti iwo anapita ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha. Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
For they have gone up to Assyria like a wild donkey alone by himself. Ephraim has hired lovers.
10 Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu, Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi. Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.
Yea, though they hire among the nations, I will now gather them, and they shall begin to be diminished because of the burden of the king of rulers.
11 “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo, maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.
Because Ephraim has multiplied altars for sinning, altars have been to him for sinning.
12 Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga, koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.
I wrote for him the multitude of my law, but they are counted as a strange thing.
13 Amapereka nsembe za nyama kwa Ine ndipo iwo amadya nyamayo, koma Yehova sakondwera nazo. Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo: iwowo adzabwerera ku Igupto.
As for the sacrifices of my offerings, they sacrifice flesh and eat it, but Jehovah does not accept them. He will now remember their iniquity, and visit their sins. They shall return to Egypt.
14 Israeli wayiwala Mlengi wake ndipo wamanga nyumba zaufumu; Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo, moto umene udzatenthe malinga awo.”
For Israel has forgotten his maker, and built palaces. And Judah has multiplied fortified cities. But I will send a fire upon his cities, and it shall devour the castles thereof.

< Hoseya 8 >