< Hoseya 11 >

1 “Israeli ali mwana, ndinamukonda, ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto. 2 Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana iwo amandithawa kupita kutali. Ankapereka nsembe kwa Abaala ndipo ankafukiza lubani kwa mafano. 3 Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda, ndipo ndinawagwira pa mkono; koma iwo sanazindikire kuti ndine amene ndinawachiritsa. 4 Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu ndi zomangira za chikondi; ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa. 5 “Sadzabwerera ku Igupto, koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo pakuti akana kutembenuka. 6 Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo, ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo nadzathetseratu malingaliro awo. 7 Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine. Ngakhale atayitana Wammwambamwamba, sizidzatheka kuti Iye awakwezenso. 8 “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu? Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli? Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima? Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero; chifundo changa chonse chikusefukira. 9 Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa, kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu. Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu, Woyerayo pakati panu. Sindidzabwera mwaukali. 10 Iwo adzatsatira Yehova; Iye adzabangula ngati mkango. Akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo. 11 Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Igupto, ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya. Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,” akutero Yehova. 12 Efereimu wandizungulira ndi mabodza, nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo. Ndipo Yuda wawukira Mulungu, wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.

< Hoseya 11 >