< Hoseya 1 >

1 Awa ndi mawu amene Yehova anayankhula kwa Hoseya mwana wa Beeri pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda ndiponso pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Yowasi mfumu ya ku Israeli.
דבר יהוה אשר היה אל הושע בן בארי בימי עזיה יותם אחז יחזקיה מלכי יהודה--ובימי ירבעם בן יואש מלך ישראל
2 Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.”
תחלת דבר יהוה בהושע ויאמר יהוה אל הושע לך קח לך אשת זנונים וילדי זנונים--כי זנה תזנה הארץ מאחרי יהוה
3 Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.
וילך ויקח את גמר בת דבלים ותהר ותלד לו בן
4 Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli.
ויאמר יהוה אליו קרא שמו יזרעאל כי עוד מעט ופקדתי את דמי יזרעאל על בית יהוא והשבתי ממלכות בית ישראל
5 Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”
והיה ביום ההוא ושברתי את קשת ישראל בעמק יזרעאל
6 Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse.
ותהר עוד ותלד בת ויאמר לו קרא שמה לא רחמה כי לא אוסיף עוד ארחם את בית ישראל--כי נשא אשא להם
7 Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”
ואת בית יהודה ארחם והושעתים ביהוה אלהיהם ולא אושיעם בקשת ובחרב ובמלחמה בסוסים ובפרשים
8 Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna.
ותגמל את לא רחמה ותהר ותלד בן
9 Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.
ויאמר קרא שמו לא עמי כי אתם לא עמי ואנכי לא אהיה לכם
10 “Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’
והיה מספר בני ישראל כחול הים אשר לא ימד ולא יספר והיה במקום אשר יאמר להם לא עמי אתם יאמר להם בני אל חי
11 Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”
ונקבצו בני יהודה ובני ישראל יחדו ושמו להם ראש אחד ועלו מן הארץ כי גדול יום יזרעאל

< Hoseya 1 >