< Genesis 48 >

1 Patapita kanthawi Yosefe anawuzidwa kuti, “Abambo ako akudwala.” Choncho anatenga ana ake awiri aja Manase ndi Efereimu ndi kupita nawo kwa Yakobo.
And it came to pass after these things, that it was reported to Joseph, Behold, thy father is sick. And he took with him his two sons, Manasseh and Ephraim.
2 Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.
And it was reported to Jacob, saying, Behold, thy son Joseph comes to thee. And Israel strengthened himself, and sat upon the bed.
3 Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa,
And Jacob said to Joseph, God Almighty appeared to me at Luz in the land of Canaan, and blessed me,
4 nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’
and said to me, Behold, I will make thee fruitful, and multiply thee, and I will make of thee a company of peoples, and will give this land to thy seed after thee for an everlasting possession.
5 “Tsopano ana ako aamuna awiri amene anabadwa ine ndisanabwere kuno adzakhala ana anga. Efereimu ndi Manase adzakhala anga monga mmene alili Rubeni ndi Simeoni.
And now thy two sons, who were born to thee in the land of Egypt before I came to thee into Egypt, are mine, Ephraim and Manasseh, even as Reuben and Simeon, shall be mine.
6 Koma amene ati adzabadwe pambuyo pa iwowa adzakhala ako ndipo cholowa chawo chidzadziwika ndi mayina a abale awo.
And thy issue, which thou beget after them, shall be thine, they shall be called after the name of their brothers in their inheritance.
7 Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).
And as for me, when I came from Paddan, Rachel died by me in the land of Canaan on the way, when there was still some distance to come to Ephrath. And I buried her there on the way to Ephrath (the same is Bethlehem).
8 Israeli ataona ana a Yosefe anafunsa kuti, “Anyamatawa ndi a yani?”
And Israel beheld Joseph's sons, and said, Who are these?
9 Yosefe anati kwa abambo ake, “Awa ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kuno.” Ndipo Israeli anati, “Bwera nawo kuno kuti ndiwadalitse.”
And Joseph said to his father, They are my sons, whom God has given me here. And he said, Bring them, I pray thee, to me, and I will bless them.
10 Koma maso a Israeli anali ofowoka chifukwa cha kukalamba moti sankaona nʼkomwe. Tsono Yosefe anabwera nawo ana ake aja pafupi ndi abambo ake ndipo abambo ake anawapsompsona nawakumbatira.
Now the eyes of Israel were dim for age, so that he could not see. And he brought them near to him, and he kissed them, and embraced them.
11 Israeli anati kwa Yosefe, “Ine sindinali kuyembekeza kuti nʼkudzaonanso nkhope yako, ndipo tsopano Mulungu wandilola kuti ndionenso ngakhale ana ako.”
And Israel said to Joseph, I had not thought to see thy face, and, lo, God has let me see thy seed also.
12 Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi.
And Joseph brought them out from between his knees, and he bowed himself with his face to the earth.
13 Yosefe anawagwira ana onse awiri padzanja, Efereimu ku dzanja lake lamanja kulunjika dzanja lamanzere la Israeli ndipo Manase ku dzanja lamanzere kulunjikitsa dzanja lamanja la Israeli, ndipo anawayandikiza kwa Yakobo.
And Joseph took them both, Ephraim in his right hand toward Israel's left hand, and Manasseh in his left hand toward Israel's right hand, and brought them near to him.
14 Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba.
And Israel stretched out his right hand, and laid it upon Ephraim's head, who was the younger, and his left hand upon Manasseh's head, guiding his hands deliberately, for Manasseh was the firstborn.
15 Kenaka anadalitsa Yosefe nati, “Mulungu amene makolo anga Abrahamu ndi Isake anamutumikira, Mulungu amene wakhala ali mʼbusa wanga moyo wanga wonse kufikira lero,
And he blessed Joseph, and said, The God before whom my fathers Abraham and Isaac walked, the God who has fed me all my life long to this day,
16 mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse, ameneyo adalitse anyamata awa. Kudzera mwa iwowa dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka. Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu pa dziko lapansi.”
the agent who has redeemed me from all evil, bless the lads, and let my name be named on them, and the name of my fathers Abraham and Isaac, and let them grow into a multitude in the midst of the earth.
17 Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase,
And when Joseph saw that his father laid his right hand upon the head of Ephraim, it displeased him. And he held up his father's hand, to remove it from Ephraim's head to Manasseh's head.
18 nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”
And Joseph said to his father, Not so, my father, for this is the firstborn, put thy right hand upon his head.
19 Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.”
And his father refused, and said, I know, my son, I know. He also shall become a people, and he also shall be great. However, his younger brother shall be greater than he, and his seed shall become a multitude of nations.
20 Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati, “Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati: Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.” Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase.
And he blessed them that day, saying, In thee will Israel bless, saying, God make thee as Ephraim and as Manasseh. And he set Ephraim before Manasseh.
21 Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu.
And Israel said to Joseph, Behold, I die, but God will be with you, and bring you again to the land of your fathers.
22 Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.”
Moreover I have given to thee one portion above thy brothers, which I took out of the hand of the Amorite with my sword and with my bow.

< Genesis 48 >