< Deuteronomo 1 >

1 Awa ndi mawu amene Mose anayankhula kwa Aisraeli onse mʼchipululu kummawa kwa Yorodani, ku Araba moyangʼanana ndi Sufi, pakati pa Parani ndi Tofeli, Labani, Heziroti ndi Dizahabu.
These are the words which Moses said to all Israel on the far side of Jordan, in the waste land in the Arabah opposite Suph, between Paran on the one side, and Tophel, Laban, Hazeroth, and Dizahab on the other.
2 (Kuyenda kuchokera ku Horebu kukafika ku Kadesi Barinea kudzera njira ya ku Phiri la Seiri ndi ulendo wa masiku khumi ndi limodzi).
It is eleven days' journey from Horeb by the way of Mount Seir to Kadesh-barnea.
3 Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo.
Now in the fortieth year, on the first day of the eleventh month, Moses gave to the children of Israel all the orders which the Lord had given him for them;
4 Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni, ndipo pa Ederi anagonjetsa Ogi mfumu ya ku Basani, amene amalamulira mu Asiteroti.
After he had overcome Sihon, king of the Amorites, ruling in Heshbon, and Og, king of Bashan, ruling in Ashtaroth, at Edrei:
5 Chakummawa kwa Yorodani mʼchigawo cha Mowabu, Mose anayamba kufotokozera lamulo ili kunena kuti:
On the far side of Jordan in the land of Moab, Moses gave the people this law, saying,
6 Ku Horebu, Yehova Mulungu wathu anati kwa ife, “Mwakhalitsa pa phiri lino.
The Lord our God said to us in Horeb, You have been long enough in this mountain:
7 Sasulani msasa ndipo pitani ku dziko la mapiri la Aamori. Pitani kwa anthu onse oyandikana nawo ku Araba, ku mapiri, mʼmbali mwa mapiri a ku madzulo, ku Negevi ndiponso mʼmbali mwa nyanja, ku dziko la Akanaani ndi ku Lebanoni mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Make a move now, and go on your way into the hill-country of the Amorites and the places near it, in the Arabah and the hill-country and in the lowlands and in the South and by the seaside, all the land of the Canaanites, and Lebanon, as far as the great river, the river Euphrates.
8 Taonani, Ine ndakupatsani dziko ili. Lowani ndi kulilanda dziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo komanso kwa zidzukulu zawo.”
See, all the land is before you: go in and take for yourselves the land which the Lord gave by an oath to your fathers, Abraham, Isaac, and Jacob, and to their seed after them.
9 Pa nthawi imeneyi ine ndinati kwa inu, “Inu ndinu katundu olemera kwambiri woti sindingathe kumunyamula ndekha.
At that time I said to you, I am not able to undertake the care of you by myself;
10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani kotero kuti lero lino ndinu ochuluka ngati nyenyezi za kumwamba.
The Lord your God has given you increase, and now you are like the stars of heaven in number.
11 Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera!
May the Lord, the God of your fathers, make you a thousand times greater in number than you are, and give you his blessing as he has said!
12 Koma nanga ndekha ndidzasenza bwanji zovuta ndi zipsinjo zanu komanso milandu yanu?
How is it possible for me by myself to be responsible for you, and undertake the weight of all your troubles and your arguments?
13 Sankhani amuna ena anzeru, ozindikira ndi amene mumawalemekeza kuchokera ku mtundu uliwonse wa mitundu yanu, ndipo ndidzawayika kuti akulamulireni.”
Take for yourselves men who are wise, far-seeing, and respected among you, from your tribes, and I will make them rulers over you.
14 Inu munandiyankha kuti, “Maganizo amenewa ndi abwino kuwachita.”
And you made answer and said to me, It is good for us to do as you say.
15 Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko.
So I took the heads of your tribes, wise men and respected, and made them rulers over you, captains of thousands and captains of hundreds and captains of fifties and captains of tens, and overseers of your tribes.
16 Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo.
And at that time I gave orders to your judges, saying, Let all questions between your brothers come before you for hearing, and give decisions uprightly between a man and his brother or one from another nation who is with him.
17 Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.”
In judging, do not let a man's position have any weight with you; give hearing equally to small and great; have no fear of any man, for it is God who is judge: and any cause in which you are not able to give a decision, you are to put before me and I will give it a hearing.
18 Ndipo nthawi imeneyo ndinakuwuzani chilichonse chimene munayenera kuchita.
And at that time I gave you all the orders which you were to do.
19 Tsono monga Yehova Mulungu wathu anatilamulira, tinanyamuka kuchoka ku Horebu ndi kupita cha ku dziko lamapiri la Aamori kudzera ku chipululu chachikulu ndi choopsa chija munachionachi, kotero kuti tinakafika ku Kadesi Barinea.
Then we went on from Horeb, through all that great and cruel waste which you saw, on our way to the hill-country of the Amorites, as the Lord gave us orders; and we came to Kadesh-barnea.
20 Ndipo ndinati kwa inu, “Mwafika ku dziko la mapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.
And I said to you, You have come to the hill-country of the Amorites, which the Lord our God is giving us.
21 Taonani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani ndi kulitenga monga Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuwuzirani. Musaope kapenanso kugwa mphwayi.”
See now, the Lord your God has put the land into your hands: go up and take it, as the Lord, the God of your fathers, has said to you; have no fear and do not be troubled.
22 Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.”
And you came near to me, every one of you, and said, Let us send men before us to go through the land with care and give us an account of the way we are to go and the towns to which we will come.
23 Ndinaona kuti maganizo amenewa anali abwino, choncho ndinasankha anthu khumi ndi awiri, mmodzi ku fuko lililonse.
And what you said seemed good to me, and I took twelve men from among you, one from every tribe;
24 Iwo ananyamuka napita mʼdziko la mapiri, ndipo anafika ku Chigwa cha Esikolo ndi kukazonda dzikolo.
And they went up into the hill-country and came to the valley of Eshcol, and saw what was there.
25 Pobwerera anatitengerako zipatso za mʼdzikomo ndipo anatipatsa mawu akuti, “Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.”
And taking in their hands some of the fruit of the land, they came down again to us, and gave us their account, saying, It is a good land which the Lord our God is giving us.
26 Koma inu simunafune kupitako ndipo munawukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.
But going against the order of the Lord your God, you would not go up:
27 Inu munanyinyirika mʼmatenti anu nʼkumati, “Mulungu amatida nʼchifukwa chake anatitulutsa ku Igupto kuti atipereke mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge.
And you made an angry outcry in your tents, and said, In his hate for us the Lord has taken us out of the land of Egypt, to give us up into the hands of the Amorites for our destruction.
28 Tigwire mtengo wanji? Abale athu anatitayitsa mtima. Iwo akuti, ‘Anthuwo ndi amphamvu ndi aatali kuposa ife, mizindayo ndi yayikulu ndipo mipanda yake ndi yayitali yofika kumwamba. Ife tinaonanso Aanaki kumeneko.’”
Where are we going up? Our brothers have made our hearts feeble with fear by saying, The people are greater and taller than we are, and the towns are great and walled up to heaven; and more than this, we have seen the sons of the Anakim there.
29 Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa.
Then I said to you, Have no fear of them.
30 Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona,
The Lord your God who goes before you will be fighting for you, and will do such wonders as he did for you in Egypt before your eyes;
31 ndi mʼchipululu muja. Kumeneko munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani monga abambo anyamulira mwana wawo, njira yonse yomwe munayenda mpaka munafika pamalo ano.”
And in the waste land, where you have seen how the Lord was supporting you, as a man does his son, in all your journeying till you came to this place.
32 Ngakhale zinali choncho, simunadalire Yehova Mulungu wanu
But for all this, you had no faith in the Lord your God,
33 amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo.
Who goes before you on your way, looking for a place where you may put up your tents, in fire by night, lighting up the way you are to go, and in a cloud by day.
34 Yehova atamva zimene munanena anakwiya nalumbira kuti,
And the Lord, hearing your words, was angry, and said with an oath,
35 “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu,
Truly, not one of this evil generation will see that good land which I said I would give to your fathers,
36 kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.”
But only Caleb, the son of Jephunneh, he will see it; and to him and to his children I will give the land over which his feet have gone, because he has been true to the Lord with all his heart.
37 Chifukwa cha inu, Yehova anakwiyiranso ine ndipo anati, “Iwenso sudzalowa mʼdzikomo.
And, in addition, the Lord was angry with me because of you, saying, You yourself will not go into it:
38 Koma Yoswa mwana wa Nuni amene amakuthandiza, adzalowa mʼdzikomo. Umulimbikitse chifukwa adzatsogolera Israeli kukalandira dzikolo.
Joshua, the son of Nun, your servant, he will go into the land: say to him that he is to be strong, for he will be Israel's guide into their heritage.
39 Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo.
And your little ones, who, you said, would come into strange hands, your children, who now have no knowledge of good or evil, they will go into that land, and to them I will give it and it will be theirs.
40 Koma inu, tembenukani nyamukani kulowera cha ku chipululu kutsatira njira ya ku Nyanja Yofiira.”
But as for you, go back, journeying into the waste land by the way of the Red Sea.
41 Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija.
Then you said to me, We have done evil against the Lord, we will go up to the attack, as the Lord our God has given us orders. And arming yourselves every one, you made ready to go up without care into the hill-country.
42 Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’”
And the Lord said to me, Say to them, Do not go up to the attack; for I am not among you, and you will be overcome by those who are against you.
43 Choncho ndinakuwuzani koma simunamve. Inu munawukira lamulo la Yehova ndipo mwamwano munayenda kulowa mʼdziko la mapiri.
This I said to you, but you gave no attention and went against the orders of the Lord, and in your pride went up into the hill-country.
44 Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima.
And the Amorites who were in the hill-country came out against you and put you to flight, rushing after you like bees, and overcame you in Seir, driving you even as far as Hormah.
45 Munabwererako mukulira pamaso pa Yehova, koma Iye sanalabadire kulira kwanuko ndipo sanakumvetsereni.
And you came back, weeping before the Lord; but the Lord gave no attention to your cries and did not give ear to you.
46 Pamenepo munakhala ku Kadesi masiku ambiri kwa nthawi yayitali ndithu.
So you were kept waiting in Kadesh for a long time.

< Deuteronomo 1 >