< 2 Mbiri 3 >

1 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu pa Phiri la Moriya, pamene Yehova anaonekera Davide abambo ake. Panali pabwalo lopunthirapo tirigu la Arauna Myebusi, malo amene anapereka Davide.
Then Solomon began to build the house of Jehovah at Jerusalem on mount Moriah, where Jehovah appeared to David his father, which he made ready in the place that David had appointed, in the threshing-floor of Ornan the Jebusite.
2 Iye anayamba kumanga pa tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake.
And he began to build in the second day of the second month, in the fourth year of his reign.
3 Maziko amene Solomoni anayika pomanga Nyumba ya Mulungu ndi awa: Mulitali munali mamita 27, mulifupi munali mamita asanu ndi anayi (potsata miyeso yakale).
Now these are the foundations which Solomon laid for the building of the house of God. The length by cubits after the first measure was sixty cubits, and the breadth twenty cubits.
4 Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54. Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino.
And the porch that was before the house, the length of it, according to the breadth of the house, was twenty cubits, and the height a hundred and twenty. And he overlaid it inside with pure gold.
5 Chipinda chachikulu, khoma lake anakhomera matabwa a payini ndipo analikutira ndi golide wabwino ndi kulikongoletsa ndi zithunzi za kanjedza ndi maunyolo.
And the greater house he ceiled with fir-wood, which he overlaid with fine gold, and wrought thereon palm trees and chains.
6 Iye anakongoletsa Nyumba ya Mulunguyo ndi miyala yokongola. Ndipo golide amene anagwiritsa ntchito anali golide wa ku Paravaimu.
And he garnished the house with precious stones for beauty. And the gold was gold of Parvaim.
7 Iye anakutira ndi golide mitanda ya ku denga, maferemu a zitseko, makoma ndi zitseko za Nyumba ya Mulungu, ndipo anajambula Akerubi mʼmakoma mwake.
He also overlaid the house, the beams, the thresholds, and the walls of it, and the doors of it, with gold, and engraved cherubim on the walls.
8 Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri.
And he made the most holy house; the length of it, according to the breadth of the house, was twenty cubits, and the breadth of it twenty cubits. And he overlaid it with fine gold, amounting to six hundred talents.
9 Misomali yagolide imalemera magalamu 570. Anakutanso ndi golide zipinda zapamwamba.
And the weight of the nails was fifty shekels of gold. And he overlaid the upper chambers with gold.
10 Ku Malo Opatulika Kwambiri iye anapangako Akerubi awiri achitsulo ndipo anawakuta ndi golide.
And in the most holy house he made two cherubim of image work, and they overlaid them with gold.
11 Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo.
And the wings of the cherubim were twenty cubits long; the wing of the one was five cubits, reaching to the wall of the house, and the other wing was likewise five cubits, reaching to the wing of the other cherub.
12 Chimodzimodzinso phiko la Kerubi wachiwiri linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza mbali ina ya khoma la Nyumba ya Mulungu, ndipo linalo limene linalinso loposera mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi woyamba uja.
And the wing of the other cherub was five cubits, reaching to the wall of the house, and the other wing was five cubits also, joining to the wing of the other cherub.
13 Mapiko a Akerubiwa akawatambasula amatalika mamita asanu ndi anayi. Akerubiwa anayimirira pa mapazi awo, kuyangʼana chipinda chachikulu.
The wings of these cherubim spread themselves forth twenty cubits. And they stood on their feet, and their faces were toward the house.
14 Solomoni anapanga nsalu zotchingira zobiriwira, zapepo ndi zofiira ndi nsalu zofewa zosalala, atajambulapo Akerubi.
And he made the veil of blue, and purple, and crimson, and fine linen, and wrought cherubim thereon.
15 Kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu anamangako zipilala ziwiri, zimene zonse pamodzi zinali zotalika mamita khumi ndi asanu ndi theka; chipilala chilichonse chinali ndi mutu woposera mamita awiri.
Also he made two pillars before the house of thirty-five cubits in length, and the capital that was on the top of each of them was five cubits.
16 Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja.
And he made chains in the oracle, and put them on the tops of the pillars. And he made a hundred pomegranates, and put them on the chains.
17 Solomoni anayimika nsanamirazo kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu, imodzi mbali ya kummwera ndi inayo mbali ya kumpoto. Nsanamira ya kummwera anayitcha Yakini ndipo ya kumpoto anayitcha Bowazi.
And he set up the pillars before the temple, one on the right hand, and the other on the left. And called the name of that on the right hand Jachin, and the name of that on the left Boaz.

< 2 Mbiri 3 >