< 1 Samueli 15 >

1 Samueli anawuza Sauli kuti, “Yehova anandituma ine kuti ndikudzozeni kukhala mfumu ya anthu ake, Aisraeli. Tsopano imvani zimene Yehova akunena.
And Samuel said to Saul, Jehovah sent me to anoint thee to be king over his people, over Israel. Now therefore hearken thou to the voice of the words of Jehovah.
2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzalanga Aamaleki chifukwa cha zimene anawachita Aisraeli. Paja iwo analimbana ndi Aisraeli pa njira pamene Aisraeliwo ankachoka ku Igupto.
Thus says Jehovah of hosts, I have remembered that which Amalek did to Israel, how he set himself against him in the way when he came up out of Egypt.
3 Tsopano pita kathire nkhondo Aamaleki ndi kuwononga kwathunthu zinthu zonse zimene ali nazo. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe. Mukaphe amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ngʼombe ndi nkhosa, ngamira ndi abulu.’”
Now go and smite Amalek, and utterly destroy all that they have, and spare them not, but kill both man and woman, infant and suckling, ox and sheep, camel and donkey.
4 Kotero Sauli anayitana ankhondo ake nawawerenga ku Telaimu. Ankhondo oyenda pansi analipo 200,000 ndipo mwa iwowa 10,000 anali a fuko la Yuda.
And Saul summoned the people, and numbered them in Telaim, two hundred thousand footmen, and ten thousand men of Judah.
5 Sauli anapita ku mzinda wa Aamaleki nawubisalira mʼkhwawa.
And Saul came to the city of Amalek, and laid wait in the valley.
6 Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.
And Saul said to the Kenites, Go, depart, get you down from among the Amalekites, lest I destroy you with them, for ye showed kindness to all the sons of Israel when they came up out of Egypt. So the Kenites departed from among the Amalekites.
7 Tsono Sauli anakantha Aamaleki kuchokera ku Havila mpaka ku Suri, kummawa kwa Igupto.
And Saul smote the Amalekites, from Havilah as thou go to Shur, that is before Egypt.
8 Sauli anatenga Agagi mfumu ya Aamaleki, koma anthu ake onse anawapha ndi lupanga.
And he took Agag the king of the Amalekites alive, and utterly destroyed all the people with the edge of the sword.
9 Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga.
But Saul and the people spared Agag, and the best of the sheep, and of the oxen, and of the fatlings, and the lambs, and all that was good, and would not utterly destroy them. But everything that was vile and refuse, that they destroyed utterly.
10 Kenaka Yehova anawuza Samueli kuti,
Then the word of Jehovah came to Samuel, saying,
11 “Ine ndikumva chisoni chifukwa ndinayika Sauli kukhala mfumu. Wabwerera mʼmbuyo, waleka kunditsata ndipo sanamvere malangizo anga.” Samueli anapsa mtima, ndipo analira kwa Yehova usiku wonse.
I regret that I have set up Saul to be king, for he has turned back from following me, and has not performed my commandments. And Samuel was angry, and he cried out to Jehovah all night.
12 Samueli anadzuka mmamawa ndipo anapita kukakumana ndi Sauli. Koma anthu anamuwuza kuti, “Sauli anabwera ku Karimeli, ndipo kumeneko wadziyimikira mwala wachikumbutso cha iye mwini. Tsopano wachokako ndipo wapita ku Giligala.”
And Samuel rose early to meet Saul in the morning, and it was told Samuel, saying, Saul came to Carmel, and, behold, he set up for him a monument, and turned, and passed on, and went down to Gilgal.
13 Samueli atamupeza Sauli, Sauliyo anati kwa Samueli, “Yehova akudalitseni! Ndachita zonse zimene Yehova analamula.”
And Samuel came to Saul. And Saul said to him, Blessed be thou of Jehovah. I have performed the commandment of Jehovah.
14 Koma Samueli anati, “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?”
And Samuel said, What then means this bleating of the sheep in my ears, and the lowing of the oxen which I hear?
15 Sauli anayankha, “Zimenezi Asilikali azitenga kuchokera kwa Aamaleki. Iwo anasungako nkhosa ndi ngʼombe zabwino kuti akapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma zina zonse anaziwononga.”
And Saul said, They have brought them from the Amalekites, for the people spared the best of the sheep and of the oxen to sacrifice to Jehovah thy God, and the rest we have utterly destroyed.
16 Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.” Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.”
Then Samuel said to Saul, Stop, and I will tell thee what Jehovah has said to me this night. And he said to him, Say on.
17 Apo Samueli anati, “Munali wamngʼono pa maso pa anthu, koma tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko a Israeli. Yehova anakudzozani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraeli.
And Samuel said, Though thou were little in thine own sight, were thou not made the head of the tribes of Israel? And Jehovah anointed thee king over Israel.
18 Ndipo Yehova anakutumani kuti, ‘Pitani mukawononge kwathunthu Aamaleki, anthu oyipa aja. Mukachite nawo nkhondo mpaka kuwatheratu.’
And Jehovah sent thee on a journey, and said, Go, and utterly destroy the sinners, the Amalekites, and fight against them until they be consumed.
19 Chifukwa chiyani simunamvere mawu a Yehova? Chifukwa chiyani munathamangira zofunkha ndi kuchita choyipira Yehova?”
Why then did thou not obey the voice of Jehovah, but did fly upon the spoil, and did that which was evil in the sight of Jehovah?
20 Koma Saulo anawuza Samueli kuti, “Ine ndinamveradi mawu a Yehova. Ndinapita kukachita zimene Yehova anandituma. Ndinabwera naye Agagi, mfumu ya Amaleki, koma Aamaleki ena onse anaphedwa.
And Saul said to Samuel, Yes, I have obeyed the voice of Jehovah, and have gone the way which Jehovah sent me, and have brought Agag the king of Amalek, and have utterly destroyed the Amalekites.
21 Koma pa zofunkhazo anthu anatengapo nkhosa, ngʼombe ndi zabwino zina zoyenera kuwonongedwa kuti akapereke ngati nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”
But the people took of the spoil, sheep and oxen, the chief of the devoted things, to sacrifice to Jehovah thy God in Gilgal.
22 Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.
And Samuel said, Has Jehovah as great delight in burnt offerings and sacrifices, as in obeying the voice of Jehovah? Behold, to obey is better than sacrifice, and to hearken than the fat of rams.
23 Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza, ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Chifukwa mwakana mawu a Yehova. Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”
For rebellion is as the sin of witchcraft, and stubbornness is as idolatry and teraphim. Because thou have rejected the word of Jehovah, he has also rejected thee from being king.
24 Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera.
And Saul said to Samuel, I have sinned, for I have transgressed the commandment of Jehovah, and thy words, because I feared the people, and obeyed their voice.
25 Tsopano ndikukupemphani, khululukireni tchimo langa ndipo mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova.”
Now therefore, I pray thee, pardon my sin, and turn again with me that I may worship Jehovah.
26 Koma Samueli anawuza Sauli kuti, “Ine sindibwerera nawe. Inu mwakana mawu a Yehova. Choncho Iyenso wakukanani kuti musakhale mfumu yolamulira Aisraeli.”
And Samuel said to Saul, I will not return with thee, for thou have rejected the word of Jehovah, and Jehovah has rejected thee from being king over Israel.
27 Samueli akutembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo unangʼambika.
And as Samuel turned about to go away, Saul laid hold upon the skirt of his robe, and it tore.
28 Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu.
And Samuel said to him, Jehovah has torn the kingdom of Israel from thee this day, and has given it to a neighbor of thine, who is better than thou.
29 Mulungu wa ulemerero wa Israeli sanama kapena kusintha maganizo ake; pakuti iye si munthu, kuti asinthe maganizo ake.”
And also the Strength of Israel will not lie nor repent, for he is not a man that he should repent.
30 Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.”
Then he said, I have sinned. Yet honor me now, I pray thee, before the elders of my people, and before Israel, and turn again with me, that I may worship Jehovah thy God.
31 Pamenepo Samueli anabwerera ndi Sauli, ndipo Sauli anapembedza Yehova.
So Samuel turned again after Saul, and Saul worshiped Jehovah.
32 Kenaka Samueli anati, “Bwera nayeni kuno Agagi, mfumu ya Amaleki ija.” Choncho Agagi anapita kwa Samueli mokondwa chifukwa ankaganiza kuti, “Ndithu zowawa za imfa zapita.”
Then Samuel said, Bring ye here to me Agag the king of the Amalekites. And Agag came to him cheerfully. And Agag said, Surely the bitterness of death is past.
33 Koma Samueli anati, “Monga momwe lupanga lako linasandutsira amayi kukhala wopanda ana, momwemonso amayi ako adzakhala opanda mwana pakati pa amayi.” Ndipo Samueli anapha Agagi pamaso pa Yehova ku Giligala.
And Samuel said, As thy sword has made women childless, so shall thy mother be childless among women. And Samuel hewed Agag in pieces before Jehovah in Gilgal.
34 Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli.
Then Samuel went to Ramah, and Saul went up to his house to Gibeah of Saul.
35 Samueli sanamuonenso Sauli mpaka imfa yake ngakhale kuti ankamulira Sauliyo. Yehova anamva chisoni kuti anasankha Sauli kuti akhale mfumu ya Israeli.
And Samuel came no more to see Saul until the day of his death, for Samuel mourned for Saul, and Jehovah regretted that he had made Saul king over Israel.

< 1 Samueli 15 >