< 1 Mafumu 8 >

1 Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide.
那時,所羅門將以色列的長老和各支派的首領,並以色列的族長,招聚到耶路撒冷,要把耶和華的約櫃從大衛城-就是錫安-運上來。
2 Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Mfumu Solomoni nthawi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiwiri.
以他念月,就是七月,在節前,以色列人都聚集到所羅門王那裏。
3 Akuluakulu onse a Israeli atafika, ansembe ananyamula Bokosi la Chipangano,
以色列長老來到,祭司便抬起約櫃,
4 ndipo anabwera nalo Bokosi la Yehova pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula,
祭司和利未人將耶和華的約櫃運上來,又將會幕和會幕的一切聖器具都帶上來。
5 ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.
所羅門王和聚集到他那裏的以色列全會眾,一同在約櫃前獻牛羊為祭,多得不可勝數。
6 Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a akerubi.
祭司將耶和華的約櫃抬進內殿,就是至聖所,放在兩個基路伯的翅膀底下。
7 Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira.
基路伯張着翅膀在約櫃之上,遮掩約櫃和抬櫃的槓。
8 Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino.
這槓甚長,槓頭在內殿前的聖所可以看見,在殿外卻不能看見,直到如今還在那裏。
9 Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
約櫃裏惟有兩塊石版,就是以色列人出埃及地後,耶和華與他們立約的時候摩西在何烈山所放的。除此以外,並無別物。
10 Ansembe atatuluka mʼMalo Opatulikawo, mtambo unadzaza Nyumba ya Yehova.
祭司從聖所出來的時候,有雲充滿耶和華的殿;
11 Ndipo ansembewo sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
甚至祭司不能站立供職,因為耶和華的榮光充滿了殿。
12 Pamenepo Solomoni anati, “Yehova anati adzakhala mʼmitambo yakuda;
那時所羅門說: 耶和華曾說, 他必住在幽暗之處。
13 taonani ndithu, ine ndakumangirani Nyumba yokongola kwambiri, malo woti muzikhalamo mpaka muyaya.”
我已經建造殿宇作你的居所, 為你永遠的住處。
14 Aisraeli onse ali chiyimire pomwepo, mfumu inatembenuka ndi kuwadalitsa.
王轉臉為以色列會眾祝福,以色列會眾就都站立。
15 Ndipo inati: “Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati,
所羅門說:「耶和華-以色列的上帝是應當稱頌的!因他親口向我父大衛所應許的,也親手成就了。
16 ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisraeli ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba, koma ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisraeli.’
他說:『自從我領我民以色列出埃及以來,我未曾在以色列各支派中選擇一城建造殿宇-為我名的居所,但揀選大衛治理我民以色列。』」
17 “Abambo anga Davide anali ndi maganizo mu mtima mwawo oti amangire nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli.
所羅門說:「我父大衛曾立意,要為耶和華-以色列上帝的名建殿。
18 Koma Yehova ananena kwa abambo anga, Davide, kuti, ‘Popeza zinali mu mtima mwako kumangira nyumba Dzina langa, unachita bwino kukhala ndi maganizo amenewa mu mtima mwakomo.
耶和華卻對我父大衛說:『你立意為我的名建殿,這意思甚好。
19 Komatu, si iwe amene udzamanga Nyumba ya Mulungu, koma mwana wako, mwana amene iwe udzabereke. Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba.’
只是你不可建殿,惟你所生的兒子必為我名建殿。』
20 “Yehova wasunga zimene analonjeza: ine ndalowa mʼmalo mwa abambo anga Davide ndipo tsopano ndili pa mpando waufumu wa Israeli, monga momwe Yehova analonjezera, ndipo ndamangira nyumba Dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
現在耶和華成就了他所應許的話,使我接續我父大衛坐以色列的國位,又為耶和華-以色列上帝的名建造了殿。
21 Ndalikonzera malo Bokosi la Chipangano mmene muli pangano la Yehova limene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa mʼdziko la Igupto.”
我也在其中為約櫃預備一處。約櫃內有耶和華的約,就是他領我們列祖出埃及地的時候,與他們所立的約。」
22 Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba,
所羅門當着以色列會眾,站在耶和華的壇前,向天舉手說:
23 nati: “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pansi pa dziko, inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.
「耶和華-以色列的上帝啊,天上地下沒有神可比你的!你向那盡心行在你面前的僕人守約施慈愛;
24 Inu mwasunga lonjezo lanu kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu. Inde zimene munalonjeza ndi pakamwa panu, mwazikwaniritsa ndi manja anu, monga mmene tikuonera lero lino.
向你僕人-我父大衛所應許的話現在應驗了。你親口應許,親手成就,正如今日一樣。
25 “Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu, pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo mokhulupirika monga iwe wachitira.’
耶和華-以色列的上帝啊,你所應許你僕人-我父大衛的話說:『你的子孫若謹慎自己的行為,在我面前行事像你所行的一樣,就不斷人坐以色列的國位。』現在求你應驗這話。
26 Ndipo tsopano, Inu Mulungu wa Israeli, lolani kuti mawu anu akwaniritsidwe amene munalonjeza mtumiki wanu Davide abambo anga.
以色列的上帝啊,求你成就向你僕人-我父大衛所應許的話。
27 “Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni, sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga!
「上帝果真住在地上嗎?看哪,天和天上的天尚且不足你居住的,何況我所建的這殿呢?
28 Koma Inu Yehova Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu lero lino.
惟求耶和華-我的上帝垂顧僕人的禱告祈求,俯聽僕人今日在你面前的祈禱呼籲。
29 Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usiku ndi usana, malo ano amene Inu munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo,’ choncho imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera akuyangʼana malo ano.
願你晝夜看顧這殿,就是你應許立為你名的居所;求你垂聽僕人向此處禱告的話。
30 Imvani pembedzero la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.
你僕人和你民以色列向此處祈禱的時候,求你在天上你的居所垂聽,垂聽而赦免。
31 “Munthu akalakwira mnzake, nawuzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lansembe la Nyumba ino,
「人若得罪鄰舍,有人叫他起誓,他來到這殿在你的壇前起誓,
32 imvani kumwambako ndi kuchitapo kanthu. Weruzani atumiki anuwo, wochimwa mugamule kuti ndi wolakwa ndipo alangidwe chifukwa cha zimene wachita. Wosachimwa mugamule kuti ndi wosalakwa, ndipo muonetse kusalakwa kwakeko.
求你在天上垂聽,判斷你的僕人:定惡人有罪,照他所行的報應在他頭上;定義人有理,照他的義賞賜他。
33 “Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani, ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera kwa Inu mʼNyumba ino,
「你的民以色列若得罪你,敗在仇敵面前,又歸向你,承認你的名,在這殿裏祈求禱告,
34 pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa makolo awo.
求你在天上垂聽,赦免你民以色列的罪,使他們歸回你賜給他們列祖之地。
35 “Pamene kumwamba kwatsekeka ndipo mvula sikugwa chifukwa anthu anu akuchimwirani, ndipo pamene apemphera akuyangʼana malo ano ndi kuvomereza Dzina lanu, ndi kutembenuka kuchoka ku machimo awo chifukwa inu mwawalanga,
「你的民因得罪你,你懲罰他們,使天閉塞不下雨;他們若向此處禱告,承認你的名,離開他們的罪,
36 pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.
求你在天上垂聽,赦免你僕人以色列民的罪,將當行的善道指教他們,且降雨在你的地,就是你賜給你民為業之地。
37 “Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene mdani wazungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera,
「國中若有饑荒、瘟疫、旱風、霉爛、蝗蟲、螞蚱,或有仇敵犯境圍困城邑,無論遭遇甚麼災禍疾病,
38 ndipo wina aliyense mwa Aisraeli akapemphera kapena kukudandaulirani, aliyense wa iwo akadziwa masautso a mu mtima mwake ndi kukweza manja awo kuloza Nyumba ino,
你的民以色列,或是眾人,或是一人,自覺有罪,向這殿舉手,無論祈求甚麼,禱告甚麼,
39 pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo chitanipo kanthu. Muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita, popeza inu mumadziwa mtima wake (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu onse),
求你在天上你的居所垂聽赦免。你是知道人心的,要照各人所行的待他們(惟有你知道世人的心),
40 motero iwo adzakuopani masiku onse amene adzakhale mʼdziko limene munalipereka kwa makolo athu.
使他們在你賜給我們列祖之地上一生一世敬畏你。
41 “Ndipo kunena za mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisraeli, koma wabwera kuchokera ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu,
「論到不屬你民以色列的外邦人,為你名從遠方而來,
42 pakuti anthu adzamva za dzina lanu lotchukali ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu, kudzapemphera akuyangʼana Nyumba ino,
(他們聽人論說你的大名和大能的手,並伸出來的膀臂)向這殿禱告,
43 pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti Nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi Dzina lanu.
求你在天上你的居所垂聽,照着外邦人所祈求的而行,使天下萬民都認識你的名,敬畏你像你的民以色列一樣;又使他們知道我建造的這殿是稱為你名下的。
44 “Pamene anthu anu apita ku nkhondo kukamenyana ndi adani awo, kulikonse kumene mungawatume, ndipo pamene apemphera kwa Yehova moyangʼana mzinda umene mwausankha ndi Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu,
「你的民若奉你的差遣,無論往何處去與仇敵爭戰,向耶和華所選擇的城與我為你名所建造的殿禱告,
45 imvani kumwambako pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo apambanitseni.
求你在天上垂聽他們的禱告祈求,使他們得勝。
46 “Pamene akuchimwirani, popeza palibe munthu amene sachimwa, ndipo Inu nʼkuwakwiyira ndi kuwapereka kwa mdani, amene adzawatenga ukapolo kupita ku dziko lake, kutali kapena pafupi;
「你的民若得罪你(世上沒有不犯罪的人),你向他們發怒,將他們交給仇敵擄到仇敵之地,或遠或近,
47 ndipo ngati asintha maganizo ali ku dziko la ukapololo ndi kulapa ndi kukudandaulirani mʼdziko la owagonjetsa ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa, tachita zinthu zoyipa,’
他們若在擄到之地想起罪來,回心轉意,懇求你說:『我們有罪了,我們悖逆了,我們作惡了』;
48 ndipo ngati abwerera kwa Inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse mʼdziko la adani awo amene anawatenga ukapolo, ndi kupemphera kwa Inu moyangʼana dziko limene munapereka kwa makolo awo, moyangʼana mzinda umene munawusankha ndiponso Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu,
他們若在擄到之地盡心盡性歸服你,又向自己的地,就是你賜給他們列祖之地和你所選擇的城,並我為你名所建造的殿禱告,
49 imvani kumwambako, malo anu wokhalamo, imvani pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo muwachitire zabwino.
求你在天上你的居所垂聽他們的禱告祈求,為他們伸冤;
50 Ndipo khululukirani anthu anu amene akuchimwirani. Khululukirani zolakwa zonse akuchitirani ndipo mufewetse mitima ya amene anawagonjetsawo kuti awachitire chifundo;
饒恕得罪你的民,赦免他們的一切過犯,使他們在擄他們的人面前蒙憐恤。
51 popeza ndi anthu anu ndiponso cholowa chanu, anthu omwe munawatulutsa ku Igupto, kuwachotsa mʼngʼanjo yamoto yosungunula zitsulo.
因為他們是你的子民,你的產業,是你從埃及領出來脫離鐵爐的。
52 “Maso anu atsekuke kuti aone dandawulo la mtumiki wanu ndiponso madandawulo a anthu anu Aisraeli, ndipo mutchere khutu nthawi iliyonse pamene akulirirani.
願你的眼目看顧僕人,聽你民以色列的祈求,無論何時向你祈求,願你垂聽。
53 Pakuti Inu munawasiyanitsa ndi anthu a mitundu ina yonse ya dziko lonse kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munanenera kudzera mwa mtumiki wanu Mose pamene Inu, Ambuye Yehova, munatulutsa makolo athu ku Igupto.”
主耶和華啊,你將他們從地上的萬民中分別出來作你的產業,是照你領我們列祖出埃及的時候,藉你僕人摩西所應許的話。」
54 Solomoni atamaliza mapemphero ndi mapembedzero onsewa kwa Yehova, anayimirira pa guwa lansembe la Yehova, nagwada atakweza manja ake kumwamba.
所羅門在耶和華的壇前屈膝跪着,向天舉手,在耶和華面前禱告祈求已畢,就起來,
55 Anayimirira ndi kudalitsa gulu lonse la Aisraeli ndi mawu okweza, nati:
站着,大聲為以色列全會眾祝福,說:
56 “Atamandike Yehova, amene wapereka mpumulo kwa anthu ake Aisraeli monga momwe analonjezera. Palibe mawu ndi amodzi omwe amene anapita pachabe pa malonjezo ake onse abwino amene anawapereka kudzera mwa mtumiki wake Mose.
「耶和華是應當稱頌的!因為他照着一切所應許的賜平安給他的民以色列人,凡藉他僕人摩西應許賜福的話,一句都沒有落空。
57 Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga momwe anakhalira ndi makolo athu; asatisiye kapena kutitaya.
願耶和華-我們的上帝與我們同在,像與我們列祖同在一樣,不撇下我們,不丟棄我們,
58 Atembenuzire mitima yathu kwa Iye, kuti tiyende mʼnjira zake zonse ndi kusunga mawu ake, malamulo ake ndi malangizo ake amene anapereka kwa makolo athu.
使我們的心歸向他,遵行他的道,謹守他吩咐我們列祖的誡命、律例、典章。
59 Ndipo mawu angawa, amene ndapemphera pamaso pa Yehova, asayiwalike pamaso pa Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, ndipo Iye alimbikitse mtumiki wake ndiponso athandize Aisraeli, anthu ake powapatsa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku,
我在耶和華面前祈求的這些話,願耶和華-我們的上帝晝夜垂念,每日為他僕人與他民以色列伸冤,
60 kotero kuti anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adziwe kuti Yehova ndi Mulungu ndipo kuti palibenso wina.
使地上的萬民都知道惟獨耶和華是上帝,並無別神。
61 Koma mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Yehova Mulungu wanu, kutsatira malamulo ake ndi kumvera malangizo ake, monga lero lino.”
所以你們當向耶和華-我們的上帝存誠實的心,遵行他的律例,謹守他的誡命,至終如今日一樣。」
62 Ndipo mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.
王和以色列眾民一同在耶和華面前獻祭。
63 Solomoni anapereka nsembe zachiyanjano kwa Yehova: ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapatula Nyumba ya Yehova.
所羅門向耶和華獻平安祭,用牛二萬二千,羊十二萬。這樣,王和以色列眾民為耶和華的殿行奉獻之禮。
64 Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo.
當日,王因耶和華殿前的銅壇太小,容不下燔祭、素祭,和平安祭牲的脂油,便將耶和華殿前院子當中分別為聖,在那裏獻燔祭、素祭,和平安祭牲的脂油。
65 Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha ku Igupto. Anachita chikondwerero chimenechi pamaso pa Yehova Mulungu wathu kwa masiku asanu ndi awiri, anawonjezerapo masiku ena asanu ndi awiri, onse pamodzi ngati masiku 14.
那時,所羅門和以色列眾人,就是從哈馬口直到埃及小河所有的以色列人,都聚集成為大會,在耶和華-我們的上帝面前守節七日又七日,共十四日。
66 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Solomoni anawuza anthu kuti apite kwawo. Anthuwo anathokoza mfumu ndipo kenaka anapita kwawo mokondwa ndi mosangalala mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira mtumiki wake Davide ndi anthu ake Aisraeli.
第八日,王遣散眾民;他們都為王祝福。因見耶和華向他僕人大衛和他民以色列所施的一切恩惠,就都心中喜樂,各歸各家去了。

< 1 Mafumu 8 >