< 1 Mafumu 6 >

1 Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.
以色列人出埃及地後四百八十年,所羅門作以色列王第四年西弗月,就是二月,開工建造耶和華的殿。
2 Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka.
所羅門王為耶和華所建的殿,長六十肘,寬二十肘,高三十肘。
3 Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka.
殿前的廊子長二十肘,與殿的寬窄一樣,闊十肘;
4 Anapanga mazenera amene maferemu ake anali olowa mʼkati mwa makoma a Nyumbayo.
又為殿做了嚴緊的窗櫺。
5 Mʼmbali mwa makoma a Nyumba yayikulu ndi chipinda chopatulika chamʼkati, anamanga zipinda zosanjikizana, mozungulira.
靠着殿牆,圍着外殿內殿,造了三層旁屋;
6 Chipinda chapansi, mulifupi mwake chinali mamita awiri, chipinda chapakati mulifupi mwake chinali mamita awiri ndi theka ndipo chipinda chapamwamba penipeni mulifupi mwake chinali mamita atatu. Iye anapanga zinthu zosongoka kunja kwa khoma la kunja kuzungulira Nyumbayo kuti asamapise kanthu pa makoma a Nyumba ya Mulungu.
下層寬五肘,中層寬六肘,上層寬七肘。殿外旁屋的樑木擱在殿牆坎上,免得插入殿牆。
7 Poyimanga Nyumbayo, anagwiritsa ntchito miyala yosemeratu, ndipo pogwira ntchitoyo sipanamveke nyundo, nkhwangwa kapena chida china chilichonse.
建殿是用山中鑿成的石頭。建殿的時候,鎚子、斧子,和別樣鐵器的響聲都沒有聽見。
8 Chipata cholowera ku chipinda chapansi chinali mbali ya kummwera kwa Nyumbayo. Panali makwerero okwerera ku chipinda chapakati ndiponso chipinda cha pamwamba.
在殿右邊當中的旁屋有門,門內有旋螺的樓梯,可以上到第二層,從第二層可以上到第三層。
9 Choncho anamanga Nyumbayo mpaka kuyimaliza ndipo denga lake linali la mitanda ndi matabwa a mkungudza.
所羅門建殿,安置香柏木的棟樑,又用香柏木板遮蓋。
10 Msinkhu wa chipinda chilichonse unali mamita awiri, ndipo anazilumukiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza.
靠着殿所造的旁屋,每層高五肘,香柏木的棟樑擱在殿牆坎上。
11 Yehova anayankhula ndi Solomoni kuti,
耶和華的話臨到所羅門說:
12 “Kunena za Nyumba imene ukumangayi, ngati iwe udzamvera malangizo anga ndi kutsatira mawu anga, ngati udzasunga malamulo anga ndi kuwachita, Ine ndidzakwaniritsa zonse zomwe ndinalonjeza Davide abambo ako.
「論到你所建的這殿,你若遵行我的律例,謹守我的典章,遵從我的一切誡命,我必向你應驗我所應許你父親大衛的話。
13 Ndipo Ine ndidzakhazikika pakati pa ana a Israeli ndipo sindidzawasiya anthu anga Aisraeli.”
我必住在以色列人中間,並不丟棄我民以色列。」
14 Kotero Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu nayimaliza.
所羅門建造殿宇。
15 Anakuta khoma la mʼkati mwake ndi matabwa a mkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku denga ndipo pansi pa Nyumbayo anayalapo matabwa a payini.
殿裏面用香柏木板貼牆,從地到棚頂都用木板遮蔽,又用松木板鋪地。
16 Kumbuyo kwa Nyumbayo anadula chipinda chachitali mamita asanu ndi anayi. Chipindachi anachimanga ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka ku denga kuti chikhale chipinda chopatulika chamʼkati mwa Nyumba ya Mulungu ngati Malo Wopatulika Kwambiri.
內殿,就是至聖所,長二十肘,從地到棚頂用香柏木板遮蔽。
17 Chipinda chachikulu chimene chinali kutsogolo kwa Malo Wopatulika Kwambiriwa, chinali mamita 18 mulitali mwake.
內殿前的外殿,長四十肘。
18 Mʼkati mwa Nyumbayi munali matabwa a mkungudza, pamene anajambulapo zithunzi za zikho ndi maluwa. Paliponse panali mkungudza wokhawokha. Panalibe mwala uliwonse umene unkaonekera.
殿裏一點石頭都不顯露,一概用香柏木遮蔽;上面刻着野瓜和初開的花。
19 Anakonza malo wopatulika mʼkati mwa Nyumbayi kuti ayikemo Bokosi la Chipangano cha Yehova.
殿裏預備了內殿,好安放耶和華的約櫃。
20 Malo wopatulika a mʼkatiwo anali a mamita asanu ndi anayi mulitali mwake, mulifupi mwake, ndi msinkhu wake. Anakuta mʼkati mwake ndi golide weniweni ndiponso anapanga guwa lansembe la matabwa a mkungudza.
內殿長二十肘,寬二十肘,高二十肘,牆面都貼上精金;又用香柏木做壇,包上精金。
21 Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide.
所羅門用精金貼了殿內的牆,又用金鍊子掛在內殿前門扇,用金包裹。
22 Motero anakuta mʼkati monse ndi golide. Anakutanso ndi golide guwa lansembe la mʼkati mwa chipinda chopatulika.
全殿都貼上金子,直到貼完;內殿前的壇,也都用金包裹。
23 Mʼchipinda chopatulika cha mʼkati anapangamo akerubi awiri a mtengo wa olivi. Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka.
他用橄欖木做兩個基路伯,各高十肘,安在內殿。
24 Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita awiri ndi theka, phiko linanso linali mamita awiri ndi theka, kutambasula mapiko awiriwo, kuchokera msonga ina mpaka msonga ina kutalika kwake kunali mamita anayi ndi theka.
這一個基路伯有兩個翅膀,各長五肘,從這翅膀尖到那翅膀尖共有十肘;
25 Kerubi wachiwiriyo msinkhu wake unalinso mamita anayi ndi theka, pakuti akerubi awiriwo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanana.
那一個基路伯的兩個翅膀也是十肘,兩個基路伯的尺寸、形像都是一樣。
26 Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka.
這基路伯高十肘,那基路伯也是如此。
27 Solomoni anayika akerubiwo mʼchipinda cha mʼkati mwenimweni mwa Nyumba ya Mulungu, atatambasula mapiko awo. Phiko la kerubi wina limakhudza khoma lina, pamene phiko la winayo limakhudza khoma linanso ndipo mapiko awo amakhudzana pakati pa chipindacho.
他將兩個基路伯安在內殿裏;基路伯的翅膀是張開的,這基路伯的一個翅膀挨着這邊的牆,那基路伯的一個翅膀挨着那邊的牆,裏邊的兩個翅膀在殿中間彼此相接;
28 Akerubiwo anawakuta ndi golide.
又用金子包裹二基路伯。
29 Pa makoma onse kuzungulira Nyumbayo, mʼzipinda za mʼkati ndi za kunja zomwe, anajambulapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa.
內殿、外殿周圍的牆上都刻着基路伯、棕樹,和初開的花。
30 Anayala golide pansi mu Nyumbamo mʼzipinda zamʼkati ndi zakunja zomwe.
內殿、外殿的地板都貼上金子。
31 Ndipo pa khomo lolowera ku malo wopatulika amʼkati anapanga zitseko za mtengo wa olivi ndipo khonde lake linali ndi mbali zisanu.
又用橄欖木製造內殿的門扇、門楣、門框;門口有牆的五分之一。
32 Ndipo pa zitseko ziwiri zija za mtengo wa olivi anajambulapo kerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa ndipo anapaka golide akerubiwo ndi mitengo ya mgwalangwayo.
在橄欖木做的兩門扇上刻着基路伯、棕樹,和初開的花,都貼上金子。
33 Anapanganso chimodzimodzi mphuthu za mbali zinayi za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo.
又用橄欖木製造外殿的門框,門口有牆的四分之一。
34 Solomoni anapanganso zitseko ziwiri za payini. Chitseko chilichonse chinali ndi mbali ziwiri zotha kuzipinda.
用松木做門兩扇。這扇分兩扇,是摺疊的;那扇分兩扇,也是摺疊的。
35 Pa zitsekozo anagobapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa wotambasuka ndipo zojambulazo anazikuta ndi golide wopyapyala.
上面刻着基路伯、棕樹,和初開的花,都用金子貼了。
36 Ndipo anamanga bwalo la mʼkati lokhala ndi khoma lokhala ndi mizere itatu ya miyala yosema ndiponso mzere umodzi wa matabwa osemedwa a mkungudza.
他又用鑿成的石頭三層、香柏木一層建築內院。
37 Maziko a Nyumba ya Yehova anamangidwa pa chaka chachinayi, mwezi wa Zivi.
所羅門 在位第四年西弗月,立了耶和華殿的根基。
38 Pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumba anatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Anamanga Nyumbayo kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
到十一年布勒月,就是八月,殿和一切屬殿的都按着樣式造成。他建殿的工夫共有七年。

< 1 Mafumu 6 >