< 1 Mafumu 22 >

1 Kwa zaka zitatu panalibe nkhondo pakati pa Aramu ndi Israeli.
They continued three years without war between Syria and Israel.
2 Koma pa chaka chachitatu, Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita kukacheza ndi mfumu ya ku Israeli.
In the third year, Jehoshaphat the king of Judah came down to the king of Israel.
3 Mfumu ya ku Israeli nʼkuti itawuza atumiki ake kuti, “Kodi inu simukudziwa kuti Ramoti Giliyadi ndi dera lathu ndipo ife palibe chimene tikuchita kuti tilitenge deralo mʼmanja mwa mfumu ya Aramu?”
The king of Israel said to his servants, “You know that Ramoth Gilead is ours, and we do nothing, and don’t take it out of the hand of the king of Syria?”
4 Tsono iye anafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane ku nkhondo ku Ramoti Giliyadi?” Yehosafati anayankha mfumu ya ku Israeli kuti, “Ine ndili monga inu, anthu anga monga anthu anu, akavalo anga monga akavalo anu.”
He said to Jehoshaphat, “Will you go with me to battle to Ramoth Gilead?” Jehoshaphat said to the king of Israel, “I am as you are, my people as your people, my horses as your horses.”
5 Koma Yehosafati anawuzanso mfumu ya ku Israeli kuti, “Poyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”
Jehoshaphat said to the king of Israel, “Please inquire first for Yahweh’s word.”
6 Choncho mfumu ya Israeli inasonkhanitsa pamodzi aneneri okwanira 400, ndipo inawafunsa kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena ndileke?” Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Ambuye waupereka mzindawo mʼmanja mwa mfumu.”
Then the king of Israel gathered the prophets together, about four hundred men, and said to them, “Should I go against Ramoth Gilead to battle, or should I refrain?” They said, “Go up; for the Lord will deliver it into the hand of the king.”
7 Koma Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi kuno kulibenso mneneri wina wa Yehova kumene ife tingakafunsireko nzeru?”
But Jehoshaphat said, “Isn’t there here a prophet of Yahweh, that we may inquire of him?”
8 Mfumu ya ku Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife tingakafunsire kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa iyeyo samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa nthawi zonse. Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu musatero.”
The king of Israel said to Jehoshaphat, “There is yet one man by whom we may inquire of Yahweh, Micaiah the son of Imlah; but I hate him, for he does not prophesy good concerning me, but evil.” Jehoshaphat said, “Don’t let the king say so.”
9 Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa atumiki ake ndipo inati, “Kayitane Mikaya mwana wa Imula msangamsanga.”
Then the king of Israel called an officer, and said, “Quickly get Micaiah the son of Imlah.”
10 Atavala mikanjo yawo yaufumu, mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopondera tirigu pafupi ndi chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.
Now the king of Israel and Jehoshaphat the king of Judah were sitting each on his throne, arrayed in their robes, in an open place at the entrance of the gate of Samaria; and all the prophets were prophesying before them.
11 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’”
Zedekiah the son of Chenaanah made himself horns of iron, and said, “Yahweh says, ‘With these you will push the Syrians, until they are consumed.’”
12 Aneneri ena onse ananenera zomwezonso. Iwo anati, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
All the prophets prophesied so, saying, “Go up to Ramoth Gilead and prosper; for Yahweh will deliver it into the hand of the king.”
13 Wamthenga amene anapita kukayitana Mikaya anamuwuza kuti, “Taonani, aneneri onse monga munthu mmodzi akunenera za kupambana kwa mfumu. Mawu anunso akhale ogwirizana ndi mawu awo, ndipo mukayankhule zabwino.”
The messenger who went to call Micaiah spoke to him, saying, “See now, the prophets declare good to the king with one mouth. Please let your word be like the word of one of them, and speak good.”
14 Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndikawawuza zokhazo zimene Yehova akandiwuze.”
Micaiah said, “As Yahweh lives, what Yahweh says to me, that I will speak.”
15 Atafika, Ahabu anamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena tileke?” Iye anayankha kuti, “Pitani ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
When he had come to the king, the king said to him, “Micaiah, shall we go to Ramoth Gilead to battle, or shall we forbear?” He answered him, “Go up and prosper; and Yahweh will deliver it into the hand of the king.”
16 Ahabu anati kwa iye, “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti undiwuze zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?”
The king said to him, “How many times do I have to adjure you that you speak to me nothing but the truth in Yahweh’s name?”
17 Pamenepo Mikaya anayankha kuti, “Ndinaona Aisraeli onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mwamtendere.’”
He said, “I saw all Israel scattered on the mountains, as sheep that have no shepherd. Yahweh said, ‘These have no master. Let them each return to his house in peace.’”
18 Mfumu ya ku Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti ameneyu samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa zokhazokha?”
The king of Israel said to Jehoshaphat, “Didn’t I tell you that he would not prophesy good concerning me, but evil?”
19 Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.
Micaiah said, “Therefore hear Yahweh’s word. I saw Yahweh sitting on his throne, and all the army of heaven standing by him on his right hand and on his left.
20 Ndipo Yehova anati, ‘Kodi ndani amene akamukope Ahabu kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi, nʼkukafera komweko?’” “Wina anapereka maganizo ena ndipo winanso maganizo ena.
Yahweh said, ‘Who will entice Ahab, that he may go up and fall at Ramoth Gilead?’ One said one thing, and another said another.
21 Potsirizira, mzimu wina unabwera ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, ‘Ine ndidzamukopa.’”
A spirit came out and stood before Yahweh, and said, ‘I will entice him.’
22 Yehova anafunsa kuti, “Ukamukopa bwanji?” Mzimuwo unati, “Ndidzapita ndi kukakhala mzimu wabodza pakamwa pa aneneri ake onse.” Yehova anati, “‘Iwe udzamukopadi. Pita kachite zomwezo.’
Yahweh said to him, ‘How?’ He said, ‘I will go out and will be a lying spirit in the mouth of all his prophets.’ He said, ‘You will entice him, and will also prevail. Go out and do so.’
23 “Ndipo tsopano taonani, Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anu onsewa. Yehova waneneratu kuti mukaona mavuto.”
Now therefore, behold, Yahweh has put a lying spirit in the mouth of all these your prophets; and Yahweh has spoken evil concerning you.”
24 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi namenya Mikaya patsaya. Iye anafunsa Mikaya kuti, “Kodi mzimu wa Yehova unadzera njira iti pamene umatuluka mwa ine kuti uziyankhula ndi iwe?”
Then Zedekiah the son of Chenaanah came near and struck Micaiah on the cheek, and said, “Which way did Yahweh’s Spirit go from me to speak to you?”
25 Mikaya anayankha kuti, “Udzaona pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”
Micaiah said, “Behold, you will see on that day when you go into an inner room to hide yourself.”
26 Pamenepo mfumu ya ku Israeli inalamula kuti, “Mugwireni Mikaya ndipo mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu
The king of Israel said, “Take Micaiah, and carry him back to Amon the governor of the city and to Joash the king’s son.
27 ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyikeni mʼndende munthu uyu ndipo musamupatse chakudya china koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwerera mwamtendere.’”
Say, ‘The king says, “Put this fellow in the prison, and feed him with bread of affliction and with water of affliction, until I come in peace.”’”
28 Mikaya ananena kuti, “Ngati mudzabwerera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo iye anapitiriza kunena kuti, “Gwiritsitsani mawu angawa, anthu inu nonse!”
Micaiah said, “If you return at all in peace, Yahweh has not spoken by me.” He said, “Listen, all you people!”
29 Choncho mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi.
So the king of Israel and Jehoshaphat the king of Judah went up to Ramoth Gilead.
30 Mfumu ya ku Israeli inawuza Yehosafati kuti, “Ine ndidzalowa mu nkhondoyi modzibisa, koma inu muvale zovala zanu zaufumu.” Choncho mfumu ya ku Israeli inadzibisa ndi kupita ku nkhondo.
The king of Israel said to Jehoshaphat, “I will disguise myself and go into the battle, but you put on your robes.” The king of Israel disguised himself and went into the battle.
31 Tsono mfumu ya ku Aramu nʼkuti italamulira anthu ake 32 olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israeli.”
Now the king of Syria had commanded the thirty-two captains of his chariots, saying, “Don’t fight with small nor great, except only with the king of Israel.”
32 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, ankaganiza kuti, “Ndithu iyi ndiye mfumu ya ku Israeli.” Choncho anabwerera kukamenyana naye, koma Yehosafati atafuwula,
When the captains of the chariots saw Jehoshaphat, they said, “Surely that is the king of Israel!” and they came over to fight against him. Jehoshaphat cried out.
33 olamulira akavalo anaona kuti sanali mfumu ya ku Israeli ndipo analeka kumuthamangitsa.
When the captains of the chariots saw that it was not the king of Israel, they turned back from pursuing him.
34 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndi kulasa mfumu ya ku Israeli polumikizira malaya ake odzitetezera. Mfumu inawuza woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka ndipo undichotse pa nkhondo pano pakuti ndalasidwa.”
A certain man drew his bow at random, and struck the king of Israel between the joints of the armor. Therefore he said to the driver of his chariot, “Turn around, and carry me out of the battle, for I am severely wounded.”
35 Nkhondo inakula kwambiri tsiku limenelo, ndipo mfumu inakhala tsonga mʼgaleta lake moyangʼanana ndi Aaramu. Magazi ake ankayenderera pansi kuchokera mʼgaleta, ndipo pa nthawi ya madzulo inamwalira.
The battle increased that day. The king was propped up in his chariot facing the Syrians, and died at evening. The blood ran out of the wound into the bottom of the chariot.
36 Pamene dzuwa linkalowa, kunamveka mfuwu wa nkhondo kuti, “Munthu aliyense apite ku mzinda wa kwawo, aliyense apite ku dziko la kwawo!”
A cry went throughout the army about the going down of the sun, saying, “Every man to his city, and every man to his country!”
37 Ndipo mfumu ija inafa, nabwera nayo ku Samariya, ndipo anayika mʼmanda kumeneko.
So the king died, and was brought to Samaria; and they buried the king in Samaria.
38 Anatsuka galeta lija pa dziwe la ku Samariya (pamene ankasamba akazi achiwerewere) ndipo agalu ananyambita magazi a mfumuyo, monga momwe Yehova ananenera.
They washed the chariot by the pool of Samaria; and the dogs licked up his blood where the prostitutes washed themselves, according to Yahweh’s word which he spoke.
39 Tsono ntchito zina za Ahabu, kuphatikiza zonse anazichita, nyumba yaufumu imene anamanga yokutidwa ndi minyanga ya njovu, mizinda yotetezedwa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
Now the rest of the acts of Ahab, and all that he did, and the ivory house which he built, and all the cities that he built, aren’t they written in the book of the chronicles of the kings of Israel?
40 Ahabu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
So Ahab slept with his fathers; and Ahaziah his son reigned in his place.
41 Yehosafati, mwana wa Asa anakhala mfumu ya ku Yuda chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya ku Israeli.
Jehoshaphat the son of Asa began to reign over Judah in the fourth year of Ahab king of Israel.
42 Yehosafati anali wa zaka 35 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Amayi ake anali Azuba mwana wa Silihi.
Jehoshaphat was thirty-five years old when he began to reign; and he reigned twenty-five years in Jerusalem. His mother’s name was Azubah the daughter of Shilhi.
43 Pa zinthu zonse, Yehosafati anayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanachite zotsutsana ndi machitidwe a abambo ake. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova. Komabe, malo azipembedzo sanawawononge, ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
He walked in all the way of Asa his father. He didn’t turn away from it, doing that which was right in Yahweh’s eyes. However, the high places were not taken away. The people still sacrificed and burned incense on the high places.
44 Yehosafati anakhala mwamtendere ndi mfumu ya ku Israeli.
Jehoshaphat made peace with the king of Israel.
45 Ntchito zake zina za Yehosafati, zinthu zimene anachita ndi zamphamvu zimene anaonetsa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Yuda?
Now the rest of the acts of Jehoshaphat, and his might that he showed, and how he fought, aren’t they written in the book of the chronicles of the kings of Judah?
46 Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zachiwerewere mwa chipembedzo amene anatsalira pa nthawi ya ulamuliro wa Asa, abambo ake.
The remnant of the sodomites, that remained in the days of his father Asa, he put away out of the land.
47 Nthawi imeneyo kunalibe mfumu ku Edomu, amene ankalamulira anali munthu woyikidwa ndi mfumu ya ku Yuda.
There was no king in Edom. A deputy ruled.
48 Yehosafati anapanga sitima zapamadzi zopita ku Ofiri kukatenga golide, koma sitimazo sizinayende chifukwa zinawonongeka ku Ezioni Geberi.
Jehoshaphat made ships of Tarshish to go to Ophir for gold, but they didn’t go, for the ships wrecked at Ezion Geber.
49 Nthawi imeneyo Ahaziya mwana wa Ahabu anawuza Yehosafati kuti, “Anthu anga ayende pa madzi pamodzi ndi anthu anu,” koma Yehosafati anakana.
Then Ahaziah the son of Ahab said to Jehoshaphat, “Let my servants go with your servants in the ships.” But Jehoshaphat would not.
50 Ndipo Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Jehoshaphat slept with his fathers, and was buried with his fathers in his father David’s city. Jehoram his son reigned in his place.
51 Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri.
Ahaziah the son of Ahab began to reign over Israel in Samaria in the seventeenth year of Jehoshaphat king of Judah, and he reigned two years over Israel.
52 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, chifukwa anayenda mʼnjira za abambo ndi amayi ake komanso mʼnjira za Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli.
He did that which was evil in Yahweh’s sight, and walked in the way of his father, and in the way of his mother, and in the way of Jeroboam the son of Nebat, in which he made Israel to sin.
53 Potumikira ndi kupembedza Baala, iye anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli, monga momwe anachitira abambo ake.
He served Baal and worshiped him, and provoked Yahweh, the God of Israel, to anger in all the ways that his father had done so.

< 1 Mafumu 22 >