< 1 Mbiri 5 >

1 Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa,
And the sons of Reuben the firstborn of Israel (for he was the firstborn, but, inasmuch as he defiled his father's couch, his birthright was given to the sons of Joseph the son of Israel, and so the genealogy is not to be reckoned after the birthright.
2 ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe)
Now Judah prevailed above his brothers, and the ruler came from him, but the birthright was Joseph's),
3 ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi.
the sons of Reuben the firstborn of Israel: Hanoch, and Pallu, Hezron, and Carmi.
4 Ana a Yoweli anali awa: Semaya, Gogi, Simei,
The sons of Joel: Shemaiah his son, Gog his son, Shimei his son,
5 Mika, Reaya, Baala,
Micah his son, Reaiah his son, Baal his son,
6 ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri.
Beerah his son, whom Tilgath-pilneser king of Assyria carried away captive. He was ruler of the Reubenites.
7 Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa: Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya,
And his brothers by their families, when the genealogy of their generations was reckoned: the chief, Jeiel, and Zechariah,
8 ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni.
and Bela the son of Azaz, the son of Shema, the son of Joel, who dwelt in Aroer, even to Nebo and Baal-meon.
9 Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi.
And eastward he dwelt even to the entrance of the wilderness from the river Euphrates, because their cattle were multiplied in the land of Gilead.
10 Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi.
And in the days of Saul they made war with the Hagrites, who fell by their hand, and they dwelt in their tents throughout all the land east of Gilead.
11 Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka:
And the sons of Gad dwelt opposite them, in the land of Bashan to Salecah:
12 Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati.
Joel the chief, and Shapham the second, and Janai, and Shaphat in Bashan.
13 Abale awo mwa mabanja awo anali awa: Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri.
And their brothers of their fathers' houses: Michael, and Meshullam, and Sheba, and Jorai, and Jacan, and Zia, and Eber, seven.
14 Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi.
These were the sons of Abihail, the son of Huri, the son of Jaroah, the son of Gilead, the son of Michael, the son of Jeshishai, the son of Jahdo, the son of Buz.
15 Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo.
Ahi the son of Abdiel, the son of Guni, was chief of their fathers' houses.
16 Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera.
And they dwelt in Gilead in Bashan, and in its towns, and in all the suburbs of Sharon, as far as their borders.
17 Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli.
All these were reckoned by genealogies in the days of Jotham king of Judah, and in the days of Jeroboam king of Israel.
18 Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo.
The sons of Reuben, and the Gadites, and the half-tribe of Manasseh, of valiant men, men able to bear buckler and sword, and to shoot with bow, and skilful in war, were forty-four thousand seven hundred and sixty, who were able to go forth to war.
19 Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu.
And they made war with the Hagrites, with Jetur, and Naphish, and Nodab.
20 Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira.
And they were helped against them, and the Hagrites were delivered into their hand, and all that were with them, for they cried to God in the battle, and he was entreated by them because they put their trust in him.
21 Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000,
And they took away their cattle: of their camels fifty thousand, and of sheep two hundred and fifty thousand, and of donkeys two thousand, and of men a hundred thousand.
22 enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo.
For there fell many slain, because the war was of God. And they dwelt in their stead until the captivity.
23 Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri.
And the sons of the half-tribe of Manasseh dwelt in the land. They increased from Bashan to Baal-hermon and Senir and mount Hermon.
24 Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo.
And these were the heads of their fathers' houses: even Epher, and Ishi, and Eliel, and Azriel, and Jeremiah, and Hodaviah, and Jahdiel, mighty men of valor, famous men, heads of their fathers' houses.
25 Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika.
And they trespassed against the God of their fathers, and played the harlot after the gods of the peoples of the land, whom God destroyed before them.
26 Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.
And the God of Israel stirred up the spirit of Pul king of Assyria, and the spirit of Tilgath-pilneser king of Assyria, and he carried them away, even the Reubenites, and the Gadites, and the half-tribe of Manasseh, and brought them to Halah, and Habor, and Hara, and to the river of Gozan to this day.

< 1 Mbiri 5 >