< 1 Mbiri 23 >

1 Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.
Now David was old and full of days; and he made Solomon his son king over Israel.
2 Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi.
He gathered together all the princes of Israel, with the priests and the Levites.
3 Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000.
The Levites were counted from thirty years old and upward; and their number by their polls, man by man, was thirty-eight thousand.
4 Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza.
David said, “Of these, twenty-four thousand were to oversee the work of Yahweh’s house, six thousand were officers and judges,
5 Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”
four thousand were doorkeepers, and four thousand praised Yahweh with the instruments which I made for giving praise.”
6 Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
David divided them into divisions according to the sons of Levi: Gershon, Kohath, and Merari.
7 Ana a Geresoni: Ladani ndi Simei.
Of the Gershonites: Ladan and Shimei.
8 Ana a Ladani: Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.
The sons of Ladan: Jehiel the chief, Zetham, and Joel, three.
9 Ana a Simei: Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu. Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.
The sons of Shimei: Shelomoth, Haziel, and Haran, three. These were the heads of the fathers’ households of Ladan.
10 Ndipo ana a Simei anali: Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya. Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.
The sons of Shimei: Jahath, Zina, Jeush, and Beriah. These four were the sons of Shimei.
11 Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.
Jahath was the chief, and Zizah the second; but Jeush and Beriah didn’t have many sons; therefore they became a fathers’ house in one reckoning.
12 Ana a Kohati: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.
The sons of Kohath: Amram, Izhar, Hebron, and Uzziel, four.
13 Ana a Amramu: Aaroni ndi Mose. Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.
The sons of Amram: Aaron and Moses; and Aaron was separated that he should sanctify the most holy things, he and his sons forever, to burn incense before Yahweh, to minister to him, and to bless in his name forever.
14 Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.
But as for Moses the man of God, his sons were named among the tribe of Levi.
15 Ana a Mose: Geresomu ndi Eliezara.
The sons of Moses: Gershom and Eliezer.
16 Zidzukulu za Geresomu: Mtsogoleri anali Subaeli.
The sons of Gershom: Shebuel the chief.
17 Zidzukulu za Eliezara: Mtsogoleri anali Rehabiya. Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.
The son of Eliezer was Rehabiah the chief; and Eliezer had no other sons, but the sons of Rehabiah were very many.
18 Ana a Izihari: Mtsogoleri anali Selomiti.
The son of Izhar: Shelomith the chief.
19 Ana a Hebroni: Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.
The sons of Hebron: Jeriah the chief, Amariah the second, Jahaziel the third, and Jekameam the fourth.
20 Ana a Uzieli: Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.
The sons of Uzziel: Micah the chief, and Isshiah the second.
21 Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Ana a Mahili: Eliezara ndi Kisi.
The sons of Merari: Mahli and Mushi. The sons of Mahli: Eleazar and Kish.
22 Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.
Eleazar died, and had no sons, but daughters only; and their relatives, the sons of Kish, took them as wives.
23 Ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.
The sons of Mushi: Mahli, Eder, and Jeremoth, three.
24 Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova.
These were the sons of Levi after their fathers’ houses, even the heads of the fathers’ houses of those who were counted individually, in the number of names by their polls, who did the work for the service of Yahweh’s house, from twenty years old and upward.
25 Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya,
For David said, “Yahweh, the God of Israel, has given rest to his people; and he dwells in Jerusalem forever.
26 sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.”
Also the Levites will no longer need to carry the tabernacle and all its vessels for its service.”
27 Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.
For by the last words of David the sons of Levi were counted, from twenty years old and upward.
28 Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu.
For their duty was to wait on the sons of Aaron for the service of Yahweh’s house—in the courts, in the rooms, and in the purifying of all holy things, even the work of the service of God’s house;
29 Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake.
for the show bread also, and for the fine flour for a meal offering, whether of unleavened wafers, or of that which is baked in the pan, or of that which is soaked, and for all measurements of quantity and size;
30 Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo,
and to stand every morning to thank and praise Yahweh, and likewise in the evening;
31 ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.
and to offer all burnt offerings to Yahweh on the Sabbaths, on the new moons, and on the set feasts, in number according to the ordinance concerning them, continually before Yahweh;
32 Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.
and that they should keep the duty of the Tent of Meeting, the duty of the holy place, and the duty of the sons of Aaron their brothers for the service of Yahweh’s house.

< 1 Mbiri 23 >