< ԳՈՐԾՔ ԱՌԱՔԵԼՈՑ 14 >

1 Իկոնիոնի մէջ՝ անոնք միասին մտան Հրեաներուն ժողովարանը, ու ա՛յնպէս խօսեցան՝ որ Հրեաներու եւ Յոյներու մեծ բազմութիւն մը հաւատաց:
Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira.
2 Բայց չհնազանդող Հրեաները՝ դրդեցին հեթանոսները, եւ անոնց անձերը չարութեան գրգռեցին եղբայրներուն դէմ:
Koma Ayuda amene anakana kukhulupirira anawutsa anthu a mitundu ina nawononga maganizo awo kutsutsana ndi abale.
3 Իսկ անոնք երկար ժամանակ հոն կենալով՝ համարձակութեամբ կը քարոզէին Տէրոջմով, որ իր շնորհքի խօսքին վկայութիւն կու տար՝ թոյլատրելով որ նշաններ եւ սքանչելիքներ կատարուին անոնց ձեռքով:
Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo.
4 Քաղաքին բազմութիւնը բաժնուեցաւ. մաս մը բռնեց Հրեաներուն կողմը, մաս մըն ալ՝ առաքեալներուն:
Anthu a mu mzindamo anagawikana; ena anali mbali ya Ayuda, ena mbali ya atumwi.
5 Երբ հեթանոսներն ու Հրեաները՝ իրենց պետերով՝ յարձակեցան, որ նախատեն եւ քարկոծեն զանոնք,
Pamenepo anthu a mitundu ina ndi Ayuda, pamodzi ndi atsogoleri awo anakonza chiwembu choti azunze atumwiwo ndi kuwagenda ndi miyala.
6 իրենք ալ՝ գիտակցելով՝ փախան Լիկայոնիայի քաղաքները, Լիւստրա ու Դերբէ եւ շրջակայքը,
Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo,
7 ու հոն կ՚աւետարանէին:
kumene anapitiriza kulalikira Uthenga Wabwino.
8 Մարդ մը նստած էր Լիւստրայի մէջ՝ անզօր ոտքերով, իր մօր որովայնէն կաղ ծնած, որ բնաւ քալած չէր:
Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake.
9 Ասիկա մտիկ կ՚ընէր Պօղոսի խօսքերը, որ ակնապիշ նայելով անոր ու նշմարելով թէ բուժուելու հաւատք ունի՝
Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho.
10 բարձրաձայն ըսաւ. «Ուղի՛ղ կանգնէ ոտքերուդ վրայ»: Ան ալ ցատկեց եւ քալեց:
Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda.
11 Երբ բազմութիւնը տեսաւ Պօղոսի ըրածը, բարձրացնելով իրենց ձայնը՝ ըսին լիկայոներէն. «Աստուածները իջած են մեզի՝ մարդոց նմանութեամբ»:
Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!”
12 Բառնաբասը կը կոչէին Դիոս, ու Պօղոսը՝ Հերմէս, քանի որ ան էր գլխաւոր խօսողը:
Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula.
13 Իսկ Դիոսի քուրմը՝ որ քաղաքին առջեւ էր, ցուլեր եւ ծաղկեպսակներ բերելով դռներուն քով՝ կ՚ուզէր զոհ մատուցանել բազմութեան հետ:
Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.
14 Բայց երբ առաքեալները՝ Բառնաբաս ու Պօղոս՝ լսեցին, պատռեցին իրենց հանդերձները եւ դուրս ցատկեցին բազմութեան մէջ՝ աղաղակելով.
Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti,
15 «Մարդի՛կ, ինչո՞ւ այդ բաները կ՚ընէք: Մե՛նք ալ մարդիկ ենք՝ կիրքերու ենթակայ ձեզի նման, ու կ՚աւետարանենք ձեզի՝ որպէսզի այդ ունայն բաներէն դառնաք ապրող Աստուծոյ, որ ստեղծեց երկինքը, երկիրը, ծովն ու բոլոր անոնց մէջ եղածները:
“Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
16 Անցեալ սերունդներուն մէջ ան թոյլատրեց բոլոր ազգերուն՝ որ երթան իրենց ճամբաներէն:
Kale Iye analola anthu a mitundu ina yonse kutsata njira zawozawo.
17 Սակայն ինքզինք չթողուց առանց վկայութեան, բարիք ընելով, անձրեւ տալով մեզի երկինքէն, նաեւ պտղաբեր եղանակներ, ու մեր սիրտերը լեցնելով կերակուրներով եւ ուրախութեամբ»:
Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.”
18 Այս բաները ըսելով՝ հազիւ կրցան հանգստացնել բազմութիւնը, որ զոհ չմատուցանէ իրենց:
Ngakhale ndi mawu awa, anavutika kuletsa gulu la anthu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19 Սակայն Հրեաներ հասան Անտիոքէն եւ Իկոնիոնէն, համոզեցին բազմութիւնը, քարկոծեցին Պօղոսը ու քաղաքէն դուրս քաշկռտեցին՝ կարծելով թէ մեռած է:
Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa.
20 Բայց երբ աշակերտները շրջապատեցին զինք՝ կանգնեցաւ, մտաւ քաղաքը, ու հետեւեալ օրը մեկնեցաւ Դերբէ՝ Բառնաբասի հետ:
Koma ophunzira atamuzungulira, Pauloyo anayimirira nalowanso mu mzindawo. Mmawa mwake iye ndi Barnaba anachoka ndi kupita ku Derbe.
21 Այդ քաղաքին մէջ աւետարանելէ ու շատերը աշակերտելէ ետք՝ անոնք վերադարձան Լիւստրա, Իկոնիոն եւ Անտիոք,
Iwo analalikira Uthenga Wabwino mu mzindawo ndipo anthu ambiri anatembenuka mtima ndi kukhala ophunzira. Kenaka anabwerera ku Lusitra, ku Ikoniya ndi ku Antiokeya.
22 ամրացնելով աշակերտներուն անձերը եւ յորդորելով՝ որ յարատեւեն հաւատքին մէջ, ըսելով. «Շատ տառապանքով պէտք է մտնենք Աստուծոյ թագաւորութիւնը»:
Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”
23 Երբ երէցներ ձեռնադրեցին անոնց՝ ամէն եկեղեցիի մէջ, ծոմապահութեամբ աղօթելով յանձնեցին զանոնք Տէրոջ՝ որուն հաւատացած էին:
Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira.
24 Եւ անցնելով Պիսիդիայի մէջէն՝ գացին Պամփիւլիա:
Atadutsa Pisidiya, anafika ku Pamfiliya.
25 Պերգէի մէջ ալ Տէրոջ խօսքը քարոզելէ ետք՝ իջան Ատալիա,
Atalalikira Mawu ku Perga, anapita ku Ataliya.
26 անկէ ալ նաւարկեցին դէպի Անտիոք, ուրկէ Աստուծոյ շնորհքին յանձնարարուած էին այն գործին համար՝ որ կատարեցին:
Ku Ataliyako, anakwera sitima ya pamadzi kubwerera ku Antiokeya kumene anayitanidwa mwachisomo cha Mulungu kuti agwire ntchito imene tsopano anali atayitsiriza.
27 Երբ եկան, հաւաքելով եկեղեցին՝ պատմեցին ինչ որ Աստուած ըրեր էր իրենց հետ, եւ թէ հաւատքի դուռը բացեր էր հեթանոսներուն:
Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro.
28 Ու հոն երկար ժամանակ կեցան աշակերտներուն հետ:
Ndipo anakhala kumeneko ndi ophunzira nthawi yayitali.

< ԳՈՐԾՔ ԱՌԱՔԵԼՈՑ 14 >