< رُؤيا 9 >

ثُمَّ بَوَّقَ ٱلْمَلَاكُ ٱلْخَامِسُ، فَرَأَيْتُ كَوْكَبًا قَدْ سَقَطَ مِنَ ٱلسَّمَاءِ إِلَى ٱلْأَرْضِ، وَأُعْطِيَ مِفْتَاحَ بِئْرِ ٱلْهَاوِيَةِ. (Abyssos g12) ١ 1
Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya. (Abyssos g12)
فَفَتَحَ بِئْرَ ٱلْهَاوِيَةِ، فَصَعِدَ دُخَانٌ مِنَ ٱلْبِئْرِ كَدُخَانِ أَتُونٍ عَظِيمٍ، فَأَظْلَمَتِ ٱلشَّمْسُ وَٱلْجَوُّ مِنْ دُخَانِ ٱلْبِئْرِ. (Abyssos g12) ٢ 2
Nyenyeziyo itatsekula pa chidzenje chakuyacho panatuluka utsi ngati wochokera mʼngʼanjo yayikulu. Dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsi ochokera mʼdzenjemo. (Abyssos g12)
وَمِنَ ٱلدُّخَانِ خَرَجَ جَرَادٌ عَلَى ٱلْأَرْضِ، فَأُعْطِيَ سُلْطَانًا كَمَا لِعَقَارِبِ ٱلْأَرْضِ سُلْطَانٌ. ٣ 3
Ndipo mʼkati mwa utsimo munatuluka dzombe kukalowa mʼdziko lapansi ndipo linapatsidwa mphamvu zoluma ngati za zinkhanira pa dziko lapansi.
وَقِيلَ لَهُ أَنْ لَا يَضُرَّ عُشْبَ ٱلْأَرْضِ، وَلَا شَيْئًا أَخْضَرَ وَلَا شَجَرَةً مَا، إِلَّا ٱلنَّاسَ فَقَطِ ٱلَّذِينَ لَيْسَ لَهُمْ خَتْمُ ٱللهِ عَلَى جِبَاهِهِمْ. ٤ 4
Dzombelo linalamulidwa kuti lisawononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu okhawo amene analibe chizindikiro cha Mulungu pa mphumi zawo.
وَأُعْطِيَ أَنْ لَا يَقْتُلَهُمْ بَلْ أَنْ يَتَعَذَّبُوا خَمْسَةَ أَشْهُرٍ. وَعَذَابُهُ كَعَذَابِ عَقْرَبٍ إِذَا لَدَغَ إِنْسَانًا. ٥ 5
Silinapatsidwe mphamvu yowapha koma yowazunza kwa miyezi isanu. Ndipo ululu umene anthuwo anawumva unali ngati wa chinkhanira chikaluma munthu.
وَفِي تِلْكَ ٱلْأَيَّامِ سَيَطْلُبُ ٱلنَّاسُ ٱلْمَوْتَ وَلَا يَجِدُونَهُ، وَيَرْغَبُونَ أَنْ يَمُوتُوا فَيَهْرُبُ ٱلْمَوْتُ مِنْهُمْ. ٦ 6
Masiku amenewo anthu adzafunafuna imfa koma sadzayipeza. Adzalakalaka kufa koma imfa izidzawathawa.
وَشَكْلُ ٱلْجَرَادِ شِبْهُ خَيْلٍ مُهَيَّأَةٍ لِلْحَرْبِ، وَعَلَى رُؤُوسِهَا كَأَكَالِيلِ شِبْهِ ٱلذَّهَبِ، وَوُجُوهُهَا كَوُجُوهِ ٱلنَّاسِ. ٧ 7
Dzombe linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali ngati zipewa zaufumu zagolide ndipo nkhope zawo ngati za anthu.
وَكَانَ لَهَا شَعْرٌ كَشَعْرِ ٱلنِّسَاءِ، وَكَانَتْ أَسْنَانُهَا كَأَسْنَانِ ٱلْأُسُودِ، ٨ 8
Tsitsi lawo linali ngati la amayi, mano awo ngati a mikango.
وَكَانَ لَهَا دُرُوعٌ كَدُرُوعٍ مِنْ حَدِيدٍ، وَصَوْتُ أَجْنِحَتِهَا كَصَوْتِ مَرْكَبَاتِ خَيْلٍ كَثِيرَةٍ تَجْرِي إِلَى قِتَالٍ. ٩ 9
Dzombelo linavala za pachifuwa zachitsulo. Phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo.
وَلَهَا أَذْنَابٌ شِبْهُ ٱلْعَقَارِبِ، وَكَانَتْ فِي أَذْنَابِهَا حُمَاتٌ، وَسُلْطَانُهَا أَنْ تُؤْذِيَ ٱلنَّاسَ خَمْسَةَ أَشْهُرٍ. ١٠ 10
Linali ndi michira ngati zinkhanira ndi mbola. Mʼmichira yake munali mphamvu yozunza nayo anthu kwa miyezi isanu.
وَلَهَا مَلَاكُ ٱلْهَاوِيَةِ مَلِكًا عَلَيْهَا، ٱسْمُهُ بِٱلْعِبْرَانِيَّةِ «أَبَدُّونَ»، وَلَهُ بِٱلْيُونَانِيَّةِ ٱسْمُ «أَبُولِّيُّونَ». (Abyssos g12) ١١ 11
Mfumu yawo inali mngelo wolamulira Chidzenje chakuya chija. Mʼchihebri dzina lake ndi Abadoni ndipo mʼChigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, Wowononga). (Abyssos g12)
ٱلْوَيْلُ ٱلْوَاحِدُ مَضَى هُوَذَا يَأْتِي وَيْلَانِ أَيْضًا بَعْدَ هَذَا. ١٢ 12
Tsoka loyamba lapita; matsoka ena awiri akubwerabe.
ثُمَّ بَوَّقَ ٱلْمَلَاكُ ٱلسَّادِسُ، فَسَمِعْتُ صَوْتًا وَاحِدًا مِنْ أَرْبَعَةِ قُرُونِ مَذْبَحِ ٱلذَّهَبِ ٱلَّذِي أَمَامَ ٱللهِ، ١٣ 13
Mngelo wachisanu ndi chimodzi anayimba lipenga lake, ndipo ndinamva liwu lochokera ku ngodya zinayi za guwa lansembe lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu.
قَائِلًا لِلْمَلَاكِ ٱلسَّادِسِ ٱلَّذِي مَعَهُ ٱلْبُوقُ: «فُكَّ ٱلْأَرْبَعَةَ ٱلْمَلَائِكَةَ ٱلْمُقَيَّدِينَ عِنْدَ ٱلنَّهْرِ ٱلْعَظِيمِ ٱلْفُرَاتِ». ١٤ 14
Liwulo linati kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi amene anali ndi lipenga uja, “Masula angelo anayi amene anamangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.”
فَٱنْفَكَّ ٱلْأَرْبَعَةُ ٱلْمَلَائِكَةُ ٱلْمُعَدُّونَ لِلسَّاعَةِ وَٱلْيَوْمِ وَٱلشَّهْرِ وَٱلسَّنَةِ، لِكَيْ يَقْتُلُوا ثُلْثَ ٱلنَّاسِ. ١٥ 15
Ndipo anamasulidwadi angelo anayi aja amene anasungidwa kukonzekera ora ili, tsiku ili, mwezi uwu ndi chaka ichi kuti aphe limodzi la magawo atatu a anthu.
وَعَدَدُ جُيُوشِ ٱلْفُرْسَانِ مِئَتَا أَلْفِ أَلْفٍ وَأَنَا سَمِعْتُ عَدَدَهُمْ. ١٦ 16
Ndinamva chiwerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali 200 miliyoni.
وَهَكَذَا رَأَيْتُ ٱلْخَيْلَ فِي ٱلرُّؤْيَا وَٱلْجَالِسِينَ عَلَيْهَا، لَهُمْ دُرُوعٌ نَارِيَّةٌ وَأَسْمَانْجُونِيَّةٌ وَكِبْرِيتِيَّةٌ، وَرُؤُوسُ ٱلْخَيْلِ كَرُؤُوسِ ٱلْأُسُودِ، وَمِنْ أَفْوَاهِهَا يَخْرُجُ نَارٌ وَدُخَانٌ وَكِبْرِيتٌ. ١٧ 17
Akavalo ndi okwerapo amene ndinaona mʼmasomphenya anga ankaoneka motere: Zovala za pachifukwa pawo zinali zofiira ngati moto, zobiriwira ngati utsi, ndi zachikasu ngati miyala ya sulufule. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango ndipo mʼkamwa mwawo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule.
مِنْ هَذِهِ ٱلثَّلَاثَةِ قُتِلَ ثُلْثُ ٱلنَّاسِ، مِنَ ٱلنَّارِ وَٱلدُّخَانِ وَٱلْكِبْرِيتِ ٱلْخَارِجَةِ مِنْ أَفْوَاهِهَا، ١٨ 18
Gawo limodzi la magawo atatu a anthu linaphedwa ndi miliri yamoto, utsi ndi sulufule zimene zinkachoka mʼkamwa mwawo.
فَإِنَّ سُلْطَانَهَا هُوَ فِي أَفْوَاهِهَا وَفِي أَذْنَابِهَا، لِأَنَّ أَذْنَابَهَا شِبْهُ ٱلْحَيَّاتِ، وَلَهَا رُؤُوسٌ وَبِهَا تَضُرُّ. ١٩ 19
Mphamvu za akavalowo inali mʼkamwa mwawo ndi mʼmichira mwawo; pakuti michira yawo inali ngati njoka; ndi mitu imene inkalumira.
وَأَمَّا بَقِيَّةُ ٱلنَّاسِ ٱلَّذِينَ لَمْ يُقْتَلُوا بِهَذِهِ ٱلضَّرَبَاتِ، فَلَمْ يَتُوبُوا عَنْ أَعْمَالِ أَيْدِيهِمْ، حَتَّى لَا يَسْجُدُوا لِلشَّيَاطِينِ وَأَصْنَامِ ٱلذَّهَبِ وَٱلْفِضَّةِ وَٱلنُّحَاسِ وَٱلْحَجَرِ وَٱلْخَشَبِ ٱلَّتِي لَا تَسْتَطِيعُ أَنْ تُبْصِرَ وَلَا تَسْمَعَ وَلَا تَمْشِيَ، ٢٠ 20
Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula.
وَلَا تَابُوا عَنْ قَتْلِهِمْ وَلَا عَنْ سِحْرِهِمْ وَلَا عَنْ زِنَاهُمْ وَلَا عَنْ سَرِقَتِهِمْ. ٢١ 21
Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo.

< رُؤيا 9 >